30
1 “Koma tsopano akundinyoza,
ana angʼonoangʼono kwa ine,
anthu amene makolo awo sindikanawalola
kuti azithandizana ndi agalu anga kuweta nkhosa zanga.
2 Kodi mphamvu zawo ndi za phindu lanji kwa ine,
pakuti mphamvu zawo zinatha kale?
3 Anali atatheratu kuwonda ndi njala,
ankayendayenda mʼdziko lopanda madzi,
mʼchipululu usiku.
4 Ankathyola therere ndi masamba owawa,
ndipo chakudya chawo chinali mizu ya mitengo ya masache.
5 Anapirikitsidwa pakati pa anthu anzawo,
akuwakuwiza ngati kuti anali akuba.
6 Anawumirizidwa kukhala ku zigwembe za mitsinje yowuma,
pakati pa matanthwe ndi mʼmaenje a mʼnthaka.
7 Ankalira ngati nyama kuthengo
ndipo ankawunjikana pamodzi pa ziyangoyango.
8 Anali anthu achabechabe ndi wopanda dzina,
anathamangitsidwa mʼdziko.
9 “Ndipo tsopano ana awo akundiyimba nyimbo zachipongwe;
ineyo ndasanduka chisudzo chawo.
10 Iwo amanyansidwa nane ndipo amandithawa;
akandiona salephera kundilavulira mʼmaso mwangamu.
11 Tsopano pakuti Mulungu wakhwefula uta wanga ndipo wandisautsa,
iwowo analekeratu kundiopa.
12 Ku dzanja langa lamanja anthu akulimbana nane;
andikumbira dzenje loti ndigweremo ndikamayenda,
andipangira mitumbira ya nkhondo kuti alimbane nane.
13 Iwo anditsekera njira;
akufuna kundichititsa ngozi,
popanda wina aliyense wowaletsa.
14 Akundithamangitsa ngati madzi olowera pa mpanda wobowoka,
iwo akubwererabwerera pakati pa chipasupasu.
15 Zoopsa zandithetsa mphamvu;
ulemu wanga wachita ngati wauluzika ndi mphepo,
chuma changa chija chazimirira ngati mtambo.
16 “Ndipo tsopano mtima wanga wachokamo;
ndili mʼmasiku amasautso.
17 Mafupa anga akuphwanya usiku pakuti
zowawa zanga sizikuleka.
18 Mʼmphamvu zake Mulungu wakhala ngati chovala changa;
Iye wandigwira ngati chovala chondithina pa khosi.
19 Wandiponya mʼmatope,
ndipo ndasanduka ngati fumbi ndi phulusa.
20 “Inu Mulungu, ine ndikulirira kwa Inu, koma simukundiyankha;
ndikayimirira, Inu simundiyangʼana nʼkomwe.
21 Inuyo mumandichitira zankhanza;
mumandizunza ndi dzanja lanu lamphamvu.
22 Mwandinyamulira ku mphepo ndipo mwandiwulutsa ndi mphepoyo;
mwandiponya mʼmphepo ya mkuntho.
23 Ndikudziwa kuti Inu mudzandifikitsa ku imfa,
kumalo kumene amoyo onse adzapitako.
24 “Ndithudi palibe munthu amene amalanga munthu wosweka mtima,
amene akupempha thandizo mʼmasautso ake.
25 Kodi ine sindinalire nawo iwo amene anali pamavuto?
Kodi mtima wanga sunamvere chisoni anthu osauka?
26 Koma pamene ndinkayembekezera zabwino, zoyipa ndiye zinandigwera;
pamene ndinkafunafuna kuwala, mdima ndiye unandigwera.
27 Kuwawa kwa mʼkati mwanga sikukuleka;
ndili mʼmasiku amasautso.
28 Ndikuyenda wothimbirira, komatu osati ndi dzuwa;
ndimayimirira pa msonkhano ndi kupempha chithandizo molira.
29 Ndasanduka mʼbale wa nkhandwe,
mnzawo wa akadzidzi.
30 Khungu langa layamba kuda ndipo likufunduka;
thupi langa likutentha chifukwa cha kuphwanya kwa thupi.
31 Pangwe wanga wasanduka woyimbira maliro,
ndipo chitoliro changa chikuyimbira anthu olira.