12
Yesu Chitsanzo Chathu
1 Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. 2 Tiyeni tiyangʼanitsitse Yesu, amene ndi woyamba ndi wotsiriza wa chikhulupiriro chathu. Chifukwa cha chimwemwe chimene chimamudikira anapirira zowawa zapamtanda. Iye ananyoza manyazi a imfa yotere ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu. 3 Muzilingalira za Iye amene anapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafowoke ndi kutaya mtima. 4 Polimbana ndi uchimo, simunafike mpaka pokhetsa magazi.
Mulungu Amalanga Ana ake
5 Kodi mwayiwala mawu olimbitsa mtima aja, amene Mulungu anayankhula kwa inu ngati ana ake? Mawuwo ndi awa:
“Mwana wanga, usapeputse kulanga kwa Ambuye
ndipo usataye mtima pamene akukudzudzula.
6 Chifukwa Ambuye amadzudzula amene amawakonda
ndipo amalanga aliyense amene amamulandira.”
7 Pamene mukupirira masautso monga chilango, Mulungu achitira inu monga ana ake. Kodi ndi mwana wotani amene abambo ake samulanga? 8 Ngati inu simulangidwa, komatu aliyense amalangidwa, ndiye kuti sindinu ana enieni koma amʼchigololo. 9 Komanso, tonsefe tinali ndi abambo athu otibala amene amatilanga ndipo timawapatsa ulemu. Nanga kodi sitidzagonjera Atate a mizimu yathu kuti tikhale ndi moyo? 10 Abambo athu ankatilanga kwa kanthawi kochepa monga amaonera kufunika kwake, koma Mulungu amatilanga kuti tipindule, kuti tikhale oyera mtima. 11 Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.
12 Nʼchifukwa chake limbitsani manja anu otopa ndi mawondo anu ogowoka. 13 Muziyenda mʼnjira zowongoka, kuti iwo amene akukutsatirani ngakhale ndi olumala ndi ofowoka asapunthwe ndi kugwa koma adzilimbikitsidwa.
Chenjezo kwa Okana Mulungu
14 Yesetsani kukhala pa mtendere ndi anthu onse ndi kukhala oyera mtima, pakuti popanda chiyero palibe ndi mmodzi yemwe adzaona Ambuye. 15 Yangʼanitsitsani kuti wina aliyense asachiphonye chisomo cha Mulungu ndiponso kuti pasaphuke muzu wamkwiyo umene udzabweretsa mavuto ndi kudetsa ambiri. 16 Yangʼanitsitsani kuti pasakhale wina wachigololo. Kapena wosapembedza ngati Esau, amene chifukwa cha chakudya cha kamodzi kokha anagulitsa ukulu wake. 17 Monga inu mukudziwa, pambuyo pake pamene anafuna kuti adalitsidwe anakanidwa. Sanapezenso mpata woti asinthe maganizo, ngakhale anafuna madalitsowo ndi misozi.
18 Inu simunafike ku phiri limene mungathe kulikhudza, loyaka moto wa mdima bii, la mphepo yamkuntho; 19 limene pali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mawu. Anthu amene amamva mawuwo anapempha kuti asawayankhulenso mawu ena. 20 Iwo anachita mantha ndi lamulo lija lakuti, “Ngakhale nyama ikangokhudza phirilo, iphedwe ndi miyala.” 21 Maonekedwenso a Mose anali woopsa kwambiri, ngakhale Mose yemwe anati, “Ine ndinachita mantha ndi kunjenjemera.”
22 Koma inu mwafika ku Phiri la Ziyoni, ku mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba. Mwafika mu msonkhano wa angelo osangalala osawerengeka. 23 Mwafika mu mpingo wa ana oyamba kubadwa, amene mayina awo analembedwa kumwamba. Inu mwafika kwa Mulungu, woweruza anthu onse, ndiponso kwa mizimu ya anthu olungama ndi osandutsidwa kukhala angwiro. 24 Kwa Yesu mʼkhalapakati wa pangano latsopano, ndiponso mwafika ku magazi owazidwa amene amayankhula mawu abwino kuposa magazi a Abele.
25 Chenjerani kuti musakane kumvera amene akuyankhula nanu. Anthu amene anakana kumvera iye amene anawachenjeza uja pa dziko lapansi pano, sanapulumuke ku chilango ayi, nanga tsono ife tidzapulumuka bwanji ngati tikufulatira wotichenjeza wochokera kumwamba? 26 Pa nthawiyo mawu ake anagwedeza dziko lapansi, koma tsopano Iye walonjeza kuti, “Kamodzi kenanso ndidzagwedeza osati dziko lapansi lokha komanso thambo.” 27 Mawu akuti, “Kamodzi kenanso,” akuonetsa kuchotsedwa kwa zimene zitha kugwedezeka, zonse zolengedwa, kotero kuti zimene sizingatheke kugwedezeka zitsale.
28 Popeza tikulandira ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni tikhale oyamika ndi kupembedza Mulungu movomerezeka ndi mwaulemu ndi mantha. 29 Pakuti Mulungu wathu ndi moto wonyeketsa.