Yeremiya
1
1 Mawu a Yeremiya mwana wa Hilikiya, mmodzi mwa ansembe a ku Anatoti, mʼdziko la Benjamini. 2 Mawuwa Yehova anayankhula naye mʼchaka cha 13 cha ulamuliro wa Yosiya mwana wa Amoni mfumu ya Yuda. 3 Yehova anayankhulanso naye pa nthawi yonse ya ulamuliro wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, mpaka mwezi wachisanu wa chaka cha 11 cha ufumu wa Zedekiya mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, pamene anthu a ku Yerusalemu anapita ku ukapolo.
Kuyitanidwa kwa Yeremiya
4 Yehova anayankhula nane kuti,
5 “Ndisanakuwumbe mʼmimba mwa amayi ako ndinali nditakudziwa kale,
iwe usanabadwe ndinali nditakupatula kale;
ndinakuyika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”
6 Ine ndinati, “Haa! Ambuye Yehova, ine sinditha kuyankhula; popeza ndikanali wamngʼono.”
7 Koma Yehova anandiwuza kuti, “Usanene kuti, ‘Ndikanali wamngʼono’ popeza udzapita kwa munthu aliyense kumene ndidzakutuma ndi kunena chilichonse chimene ndidzakulamulira. 8 Usawaope, pakuti Ine ndili nawe, ndipo ndidzakupulumutsa,” akutero Yehova.
9 Pamenepo Yehova anatambalitsa dzanja lake nakhudza pakamwa panga, nandiwuza kuti, “Taona, tsopano ndayika mawu anga mʼkamwa mwako. 10 Lero ndakusankha kuti ukhale ndi ulamuliro pa mitundu ya anthu ndi pa maufumu awo kuti uzule ndi kugwetsa, uwononge ndi kugumula, kuti uwamange ndi kudzala.”
11 Yehova anandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuona chiyani?”
Ine ndinayankha kuti, “Ndikuona nthambi ya mtengo wa mtowo.”
12 Yehova anandiwuza kuti, “Waona bwino, chifukwa Ine ndikuonetsetsa kuti mawu angawa akwaniritsidwe.”
13 Yehova anandifunsanso kachiwiri kuti, “Kodi ukuona chiyani?”
Ine ndinayankha kuti, “Ndikuona mʼphika wa madzi owira, ndipo wagudukira kuno kummwera.”
14 Yehova anandiwuza kuti, “Mavuto a anthu onse okhala mʼdziko lino adzachokera kumpoto. 15 Ine ndikuyitana anthu onse a ku maufumu a kumpoto,” akutero Yehova.
“Mafumu awo adzabwera ndipo aliyense adzakhazika mpando wake waufumu
polowera pa zipata za Yerusalemu;
iwo adzabwera ndi kuzungulira makoma ake
ndiponso midzi yonse ya dziko la Yuda.
16 Ndidzatulutsa mlandu wanga ndi iwo
chifukwa cha zoyipa zimene anachita pondisiya Ine.
Iwo anakafukiza lubani kwa milungu ina,
ndi kupembedza zimene anapanga ndi manja awo.
17 “Koma iwe Yeremiya konzeka! Nyamuka ndipo ukawawuze zonse zimene ndakulamulira. Usachite nawo mantha, kuopa kuti Ine ndingakuchititse mantha iwo akuona. 18 Taona, lero ndakupanga kukhala ngati mzinda wotetezedwa, ngati mzati wachitsulo ndiponso ngati makoma a mkuwa kuti usaopsedwe ndi munthu aliyense wa mʼdzikomo; kaya ndi mafumu a Yuda, akuluakulu ake, ansembe ake, kapena munthu wamba wa mʼdzikomo. 19 Iwo adzalimbana nawe koma sadzakugonjetsa, popeza Ine ndili nawe ndipo ndidzakupulumutsa,” akutero Yehova.