KALATA YA PAULO YOLEMBERA
FILEMONI
1
1 Kuchokera kwa Paulo, amene ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu ndi Timoteyo mʼbale wathu.
Kulembera Filemoni, bwenzi lathu lokondedwa ndi mtumiki mnzathu. 2 Kwa Apiya mlongo wathu, Arkipo msilikali mnzathu, ndiponso mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwanu.
3 Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi inu.
Kuyamika ndi Pemphero
4 Ine ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakukumbukira iwe mʼmapemphero anga. 5 Pakuti ndamva za chikondi chako, za chikhulupiriro chako mwa Ambuye Yesu ndiponso za chikondi chako pa oyera mtima onse. 6 Ine ndikupemphera kuti mgwirizano wako ndi ife mʼchikhulupiriro ukhale opindulitsa pozamitsa nzeru zako zozindikira zinthu zilizonse zabwino zimene timagawana chifukwa cha Khristu. 7 Mʼbale, chikondi chako chandipatsa chimwemwe chachikulu ndi chilimbikitso, chifukwa umatsitsimutsa mitima ya anthu a Ambuye.
Paulo Apempha kuti Amuchitire Chifundo Onesimo
8 Tsopano ngakhale kuti mwa Khristu nditha kulimba mtima ndi kulamulira kuti uchite zimene uyenera kuchita, 9 komabe ndikupempha mwachikondi. Ine Paulo, munthu wokalamba, ndipo tsopano ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu, 10 ndikukupempha chifukwa cha mwana wanga Onesimo, amene ndamubala ndili mu unyolo. 11 Anali wopanda phindu kwa iwe, koma tsopano wasanduka wa phindu kwa iwe ndi kwa inenso.
12 Ine ndikumutumizanso kwa iwe tsopano, koma potero ndikukhala ngati ndikutumiza mtima wanga weniweni. 13 Ndikanakonda ndikanakhala naye kuno kuti iyeyo azinditumikira mʼmalo mwako pamene ndili mu unyolo chifukwa cha Uthenga Wabwino. 14 Koma sindikufuna kuchita kanthu osakufunsa, nʼcholinga chakuti chilichonse chabwino ungandichitire chikhale mwakufuna kwako osati mokakamiza. 15 Mwina chifukwa chimene unasiyana naye kwa kanthawi ndi chakuti ukhale nayenso nthawi zonse. 16 Osati ngati kapolo, koma woposa kapolo, ngati mʼbale wokondedwa. Iyeyu ndi wokondedwa kwambiri kwa ine koma kwa iweyo ndi wokondedwa koposa, ngati munthu komanso ngati mʼbale mwa Ambuye.
17 Tsono ngati umati ndine mnzako, umulandire iyeyu monga momwe ukanandilandirira ineyo. 18 Ngati anakulakwira kapena kukongola kanthu kalikonse, ndidzalipira ineyo. 19 Ine, Paulo ndikulemba zimenezi ndi dzanja langa. Ine ndidzalipira. Nʼkosafunika kukukumbutsa kuti iweyo ngongole yako kwa ine ndi moyo wakowo. 20 Mʼbale, ndikufuna kuti ndipindule nawe mwa Ambuye; tsono tsitsimutsa mtima wanga mwa Khristu. 21 Ine ndili ndi chitsimikizo cha kumvera kwako pamene ndikukulembera kalatayi. Ndikulemba ndikudziwa kuti udzachita ngakhale kuposa zimene ndakupemphazi.
22 Chinthu chinanso ndi ichi: undikonzere malo, chifukwa ndikukhulupirira kuti Mulungu adzamvera mapemphero anu ndi kundibwezera kwa inu.
Mawu Otsiriza
23 Epafra, wamʼndende mnzanga chifukwa cha Khristu Yesu akupereka moni. 24 Atumiki anzanga awa, Marko, Aristariko, Dema ndi Luka, akuperekanso moni.
25 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wako.