Mika
1
1 Yehova anayankhula ndi Mika wa ku Moreseti pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda. Awa ndi masomphenya amene iye anaona onena za Samariya ndi Yerusalemu.
2 Tamverani, inu anthu a mitundu yonse,
mvetsera iwe dziko lapansi ndi okhala mʼmenemo,
pakuti Ambuye Yehova achitira umboni wokutsutsani,
Ambuye akuyankhula ali mʼnyumba yake yopatulika.
Chiweruzo cha Samariya ndi Yerusalemu
3 Taonani! Yehova akubwera kuchokera ku malo ake;
Iye akutsika ndipo akuponda pa malo okwera a dziko lapansi.
4 Mapiri akusungunuka pansi pake,
ndipo zigwa zikugawikana
ngati phula pa moto,
ngati madzi ochokera mʼphiri.
5 Zonsezi ndi chifukwa cha cholakwa cha Yakobo,
chifukwa cha machimo a nyumba ya Israeli.
Kodi cholakwa cha Yakobo nʼchiyani?
Kodi si Samariya?
Kodi malo achipembedzo a Yuda ndi ati?
Kodi si Yerusalemu?
6 “Choncho Ine ndidzasandutsa Samariya kukhala bwinja,
malo odzalamo mphesa.
Miyala yake ndidzayitaya ku chigwa
ndipo ndidzafukula maziko ake.
7 Mafano ake onse ndidzawaphwanyaphwanya;
mphatso zake zonse ndidzazitentha ndi moto;
ndidzawononga zifanizo zonse za milungu yake.
Popeza analandira mphatso zake kuchokera ku malipiro a akazi achiwerewere,
mphatsozonso zidzagwiritsidwa ntchito ndi ena ngati malipiro a akazi achiwerewere.”
Kulira ndi Kumva Chisoni
8 Chifukwa cha zimenezi ine ndidzalira momvetsa chisoni;
ndidzayenda wopanda nsapato ndi wamaliseche.
Ndidzafuwula ngati nkhandwe
ndi kulira ngati kadzidzi.
9 Pakuti chilonda cha Samariya nʼchosachizika;
chafika ku Yuda.
Chafika pa chipata chenicheni cha anthu anga,
mpaka mu Yerusalemu mwenimwenimo.
10 Musanene zimenezi ku Gati;
musalire nʼkomwe.
Mugubuduzike mu fumbi
ku Beti-Leafura.
11 Inu anthu okhala ku Safiro,
muzipita ku ukapolo muli amaliseche ndi amanyazi.
Iwo amene akukhala ku Zanaani
sadzatuluka.
Beti-Ezeli akulira mwachisoni;
chitetezo chake chakuchokerani.
12 Anthu amene amakhala ku Maroti akubuwula ndi ululu,
akuyembekezera thandizo,
chifukwa Yehova wabweretsa tsoka,
lafika mpaka pa chipata cha Yerusalemu.
13 Inu anthu okhala ku Lakisi
mangani akavalo ku magaleta.
Inu amene munayamba kuchimwitsa
mwana wamkazi wa Ziyoni,
pakuti zolakwa za Israeli
zinapezeka pakati panu.
14 Chifukwa chake perekani mphatso zolawirana
ndi a ku Moreseti Gati.
Mzinda wa Akizibu udzaonetsa kunama
kwa mafumu a Israeli.
15 Ndidzabweretsa mgonjetsi kudzalimbana ndi inu
okhala mu Maresa.
Ulemerero wa Israeli udzafika
ku Adulamu.
16 Metani mipala mitu yanu kuonetsa kuti mukulirira
ana anu amene mumawakonda;
mudzichititse dazi ngati dembo,
pakuti anawo adzatengedwa pakati panu kupita ku ukapolo.