BUKU LACHINAYI
90
Masalimo 90–106
Pemphero la Mose munthu wa Mulungu.
Ambuye, mwakhala muli malo athu okhalamo
pa mibado yonse.
Mapiri asanabadwe,
musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse,
kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.
 
Inu mumabwezera anthu ku fumbi,
mumati, “Bwerera ku fumbi iwe mwana wa munthu.”
Pakuti zaka 1,000 pamaso panu
zili ngati tsiku limene lapita
kapena ngati kamphindi ka usiku.
Inu mumasesa anthu mʼtulo ta imfa,
iwo ali ngati udzu watsopano wa mmawa,
ngakhale kuti mmawa umaphuka watsopano,
pofika madzulo wauma ndi kufota.
 
Ife tathedwa ndi mkwiyo wanu;
ndipo taopsezedwa ndi kuyipidwa kwanu.
Mwayika mphulupulu zathu pamaso panu,
machimo athu obisika poonekera pamaso panu.
Masiku athu onse amatha ali pansi pa ukali wanu;
timatsiriza zaka zathu ndi kubuwula.
10 Kuchuluka kwa masiku athu ndi 70,
kapena 80 ngati tili ndi mphamvu;
komabe zaka zonsezi ndi za mavuto ndi nkhawa,
zimatha mofulumira ndipo ife timawulukira kutali.
 
11 Kodi ndani amadziwa mphamvu ya mkwiyo wanu?
Pakuti ukali wanu ndi waukulu ngati ulemu umene uyenera Inu.
12 Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola,
kuti tikhale ndi mtima wanzeru.
 
13 Lezani mtima Inu Yehova! Kodi mudzatikwiyira mpaka liti?
Achitireni chifundo atumiki anu.
14 Mutikhutitse mmawa ndi chikondi chanu chosatha,
kuti tiyimbe ndi chimwemwe ndi kukhala okondwa masiku athu onse.
15 Tisangalatseni masiku ambiri monga masiku amene mwatisautsa,
kwa zaka zambiri monga momwe tinaonera mavuto.
16 Ntchito zanu zionetsedwe kwa atumiki anu,
kukongola kwanu kwa ana awo.
 
17 Kukoma mtima kwa Ambuye Mulungu wathu kukhale pa ife;
tikhazikitsireni ntchito ya manja athu;
inde, khazikitsani ntchito ya manja athu.