Salimo 74
Ndakatulo ya Asafu.
Nʼchifukwa chiyani mwatitaya ife kwamuyaya, Inu Mulungu?
Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutira pa nkhosa za busa lanu?
Kumbukirani anthu amene munawagula kalekale,
fuko la cholowa chanu, limene Inu munaliwombola,
phiri la Ziyoni, kumene inuyo mumakhala.
Tembenuzani mapazi kuloza ku mabwinja awa amuyaya
chiwonongeko ichi chonse mdani wabweretsa pa malo opatulika.
 
Adani anu anabangula pa malo pamene Inu munkakumana nafe;
anayimika mbendera zawo monga zizindikiro zachigonjetso.
Iwo anachita ngati anthu oti anyamula mbendera zawo
kuti adule mitengo mʼnkhalango.
Kenaka anaphwanya ndi nkhwangwa ndi akasemasema awo
zonse zimene tinapachika.
Iwo anatentha malo anu opatulika mpaka kuwagwetsa pansi;
anadetsa malo okhalamo dzina lanu.
Ndipo anati mʼmitima yawo, “Tawatha kwathunthu.”
Anatentha malo aliwonse amene Mulungu amapembedzedwerako mʼdzikomo.
Ife sitinapatsidwe chizindikiro chodabwitsa;
palibe aneneri amene atsala
ndipo palibe aliyense wa ife akudziwa kuti izi zidzatenga nthawi yayitali bwanji.
 
10 Kodi mpaka liti, mdani adzanyoze Inu Mulungu?
Kodi amaliwongowa adzapeputsa dzina lanu kwamuyaya?
11 Chifukwa chiyani mukubweza dzanja lanu lamanja?
Litulutseni kuchoka pachifuwa chanu ndipo muwawononge!
 
12 Koma Inu Mulungu, ndinu Mfumu yanga kuyambira kalekale;
Mumabweretsa chipulumutso pa dziko lapansi.
13 Ndinu amene munagawa nyanja ndi mphamvu yanu;
munathyola mitu ya zirombo za mʼmadzi.
14 Ndinu amene munaphwanya mitu ya Leviyatani
ndi kuyipereka ngati chakudya cha zirombo za mʼchipululu.
15 Ndinu amene munatsekula akasupe ndi mitsinje,
munawumitsa mitsinje imene siphwa nthawi zonse.
16 Masana ndi anu ndipo usiku ndi wanunso;
Inuyo munakhazikitsa dzuwa ndi mwezi.
17 Ndinu amene munakhazikitsa malire onse a dziko lapansi;
munakhazikitsa chilimwe ndi dzinja.
 
18 Kumbukirani momwe mdani wakunyozerani Inu Yehova,
momwe anthu opusa apeputsira dzina lanu.
19 Musapereke moyo wa nkhunda yanu ku zirombo zakuthengo;
nthawi zonse musayiwale miyoyo ya anthu anu osautsidwa.
20 Mukumbukire pangano lanu, pakuti malo obisika a mʼdziko
asanduka mochitira zachiwawa zochuluka.
21 Musalole kuti osautsidwa abwerere mwamanyazi;
osauka ndi osowa atamande dzina lanu.
 
22 Dzukani Inu Mulungu ndipo dzitetezeni pa mlandu;
kumbukirani momwe opusa akukunyozerani tsiku lonse.
23 Musalekerere phokoso la otsutsana nanu,
chiwawa cha adani anu, chimene chikumveka kosalekeza.