Salimo 35
Salimo la Davide.
Inu Yehova, mulimbane nawo amene akulimbana nane;
mumenyane nawo amene akumenyana nane.
Tengani chishango ndi lihawo;
dzukani ndipo bwerani mundithandize.
Tengani mkondo ndi nthungo,
kulimbana ndi iwo amene akundithamangitsa.
Uzani moyo wanga kuti,
“Ine ndine chipulumutso chako.”
 
Iwo amene akufunafuna moyo wanga
anyozedwe ndi kuchita manyazi;
iwo amene akukonza kuti moyo wanga uwonongeke
abwerere mʼmbuyo mochititsa mantha.
Akhale ngati mankhusu owuluka ndi mphepo
pamene mngelo wa Yehova akuwapirikitsa.
Njira yawo ikhale ya mdima ndi yoterera
pamene mngelo wa Yehova akuwathamangitsa.
Popeza ananditchera ukonde popanda chifukwa
ndipo popanda chifukwa andikumbira dzenje,
chiwonongeko chiwapeza modzidzimutsa
ukonde umene iwo abisa uwakole,
agwere mʼdzenje kuti awonongedwe.
Pamenepo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova
ndi kusangalala ndi chipulumutso chake.
10 Thupi langa lidzafuwula mokondwera,
“Ndani angafanane nanu Yehova?
Mumalanditsa osauka kwa amene ali ndi mphamvu zambiri,
osauka ndi osowa kwa iwo amene amawalanda.”
 
11 Mboni zopanda chisoni zinayimirira,
zinandifunsa zinthu zimene sindikuzidziwa.
12 Iwo anandibwezera zoyipa pa zabwino
ndipo anasiya moyo wanga pa chisoni.
13 Koma pamene iwo ankadwala, ine ndinavala chiguduli
ndi kudzichepetsa ndekha posala zakudya.
Pamene mapemphero anga anabwerera kwa ine osayankhidwa,
14 ndinayendayenda ndi kulira maliro,
kumulira ngati bwenzi langa kapena mʼbale wanga.
Ndinaweramitsa mutu wanga mosweka mtima
kukhala ngati ndikulira amayi anga.
15 Koma pamene ndinaphunthwa, iwo anasonkhana mosangalala;
ondithira nkhondo anasonkhana kutsutsana nane, ineyo osadziwa.
Iwo sanasiye kundiyankhulira mawu onyoza.
16 Monga anthu osapembedza, iwo anandinyoza mwachipongwe;
anandikukutira mano awo.
17 Ambuye, mpaka liti mudzakhala mukungoyangʼana?
Landitsani moyo wanga ku chiwonongeko chawo,
moyo wanga wopambana ku mikango.
18 Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu;
pakati pa gulu lalikulu la anthu ndidzakutamandani.
 
19 Musalole adani anga onyenga
akondwere chifukwa cha masautso anga;
musalole kuti amene amadana nane popanda chifukwa
andiyangʼane chamʼmbali mondinyoza.
20 Iwowo sayankhula mwamtendere,
koma amaganizira zonamizira
iwo amene amakhala mwabata mʼdziko.
21 Iwo amandiseka mofuwula ndipo amati, “Haa! Haa!
Ndipo ndi maso athuwa ife taziona.”
 
22 Yehova mwaona zimenezi; musakhale chete.
Ambuye musakhale kutali ndi ine.
23 Dzukani, ndipo nyamukani kunditeteza!
Mulimbane nawo chifukwa cha ine, Mulungu wanga ndi Ambuye anga.
24 Onetsani kusalakwa kwanga mwa chilungamo chanu, Inu Yehova Mulungu wanga.
Musalole kuti akondwere chifukwa cha mavuto anga.
25 Musalole kuti aganize kuti, “Amati atani, zachitika monga momwe timafunira!”
Kapena kunena kuti, “Tamutha ameneyu basi.”
 
26 Onse amene amakondwera ndi masautso anga
achite manyazi ndi kusokonezeka.
Onse amene amadzikweza kufuna kundipambana,
avekedwe manyazi ndi mnyozo ngati zovala.
27 Koma amene amakondwera chifukwa chakuti ndine wosalakwa,
afuwule mwachimwemwe ndi chisangalalo.
Nthawi zonse azinena kuti, “Yehova akwezeke,
Iye amene amakondwera ndi kupeza bwino kwa mtumiki wake.”
28 Pakamwa panga padzayankhula za chilungamo chanu
ndi za matamando anu tsiku lonse.