7
Miyambo ya Makolo ya Ayuda
1 Afarisi ndi ena mwa aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anasonkhana momuzungulira Yesu ndipo 2 iwo anaona ophunzira ake akudya chakudya ndi mʼmanja mwakuda kapena kuti mʼmanja mosasamba. 3 (Afarisi ndi Ayuda onse sadya pokhapokha atasamba mʼmanja, kusunga mwambo wa makolo awo. 4 Akabwera kuchokera ku msika samadya pokhapokha atasamba. Ndipo amasunga miyambo ina yambiri monga, kutsuka zikho, mitsuko ndi maketulo).
5 Choncho Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anafunsa Yesu kuti, “Nʼchifukwa chiyani ophunzira anu satsatira mwambo wa makolo, mʼmalo mwake amangodya chakudya ndi mʼmanja mwakuda?”
6 Iye anayankha kuti, “Yesaya ananena zoona pamene ananenera za inu achiphamaso; monga kunalembedwa kuti:
“Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo,
koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.
7 Amandilambira Ine kwachabe;
ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.
8 Mwasiya malamulo a Mulungu ndipo mwagwiritsitsa miyambo ya anthu.”
9 Ndipo anawawuzanso kuti, “Inu muli ndi njira yabwino yokankhira kumbali malamulo a Mulungu kuti mukatsatire miyambo yanuyo! 10 Pakuti Mose anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako,’ ndipo, ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’ 11 Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukanayenera kulandira kuchokera kwa ine ndi Korobani’ (kutanthauza kuti, mphatso yoperekedwa kwa Mulungu), 12 pamenepo inu simumalola kuti achitire kanthu kalikonse abambo kapena amayi ake. 13 Potero mumachepetsa mawu a Mulungu kukhala wopanda mphamvu ndi miyambo yanu imene mumapatsirana. Ndipo mumachita zinthu zina zambiri monga zimenezi.”
14 Yesu anayitananso gulu la anthu ndipo anati, “Tandimverani nonsenu, ndipo zindikirani izi. 15 Palibe kanthu kunja kwa munthu kamene kakalowa mwa iye kangamusandutse wodetsedwa. Koma zimene zituluka mwa munthu ndizo zimupanga kukhala wodetsedwa.” 16 (Ngati wina ali ndi makutu akumva amve).
17 Atalisiya gulu la anthu ndi kulowa mʼnyumba, ophunzira ake anamufunsa za fanizoli 18 Iye anawafunsa kuti, “Kodi nanunso simumvetsetsa? Kodi simukuona kuti palibe kanthu kamene kakalowa mwa munthu kochokera kunja kakhoza kumudetsa? 19 Pakuti sikalowa mu mtima wake koma mʼmimba mwake, ndipo kenaka kamatuluka kunja.” (Ndi mawu amenewa, Yesu anayeretsa zakudya zonse).
20 Anapitiriza kuti, “Chimene chichokera mwa munthu ndi chomwe chimamudetsa. 21 Pakuti kuchokera mʼkati mwa mitima ya anthu, mumatuluka maganizo oyipa, chiwerewere, kuba, kupha, chigololo, 22 dyera, nkhwidzi, chinyengo, machitidwe onyansa, kaduka, chipongwe, kudzikuza ndi kupusa. 23 Zoyipa zonsezi zimatuluka mʼkati ndipo zimadetsa munthu.”
Chikhulupiriro cha Mayi wa ku Siriya Fonisia
24 Yesu anachoka kumalo amenewo napita ku madera a Turo. Iye analowa mʼnyumba ndipo sanafune wina kuti adziwe zimenezi; komabe sanathe kudzibisa. 25 Kunena zoona, amayi amene kamwana kawo kakakazi kanali kogwidwa ndi mzimu woyipa, atangomva za Iye, anabwera nagwada pa mapazi ake. 26 Mayiyu anali Mhelene, wobadwira ku Fonisia wa ku Siriya. Anamupempha Yesu kuti atulutse chiwanda mwa mwana wake.
27 Iye anamuwuza kuti, “Choyamba asiye ana adye zimene akuzifuna, pakuti si kwabwino kutenga buledi wa ana ndi kuponyera agalu awo.”
28 Mayiyo anayankha kuti, “Inde Ambuye, koma ngakhale agalu amadya zomwe zimagwa pansi kuchokera pa tebulo la ana.”
29 Ndipo Iye anamuwuza kuti, “Chifukwa cha yankholi, ukhoza kupita; chiwanda chachoka mwa mwana wako wamkazi.”
30 Atapita kwawo anakapeza mwana wake aligone pa bedi, chiwanda chitatuluka.
Kuchiritsidwa kwa Munthu Wosamva ndi Wosayankhula
31 Ndipo Yesu anachoka ku dera la Turo nadutsa pakati pa Sidoni, kutsikira ku nyanja ya Galileya kupita ku dera la Dekapoli. 32 Kumeneko anthu ena anabweretsa kwa Iye munthu amene anali wosamva ndi wosayankhula, ndipo anamupempha kuti asanjike dzanja pa iye.
33 Atamutengera iye pambali, patali ndi gulu la anthu, Yesu analowetsa zala zake mʼmakutu a munthuyo. Kenaka anapaka malovu pachala ndi kukhudza lilime la munthuyo. 34 Iye anayangʼana kumwamba ndipo ndi mawu otsitsa moyo, anati kwa iye, “Efataa!” (Kutanthauza kuti, “Tsekuka!”) 35 Atachita izi, makutu a munthuyo anatsekuka komanso lilime lake linamasuka ndipo anayamba kuyankhula momveka bwino.
36 Yesu anawalamula kuti asawuze wina aliyense. Koma pamene anapitiriza kuwaletsa, iwo anapitiriza kuyankhula za izi. 37 Anthu anadabwa kwambiri. Iwo anati, “Wachita zonse bwino, ngakhale Iyenso atsekula makutu a osamva ndi osayankhula kuti ayankhule.”