11
Otumidwa ndi Yohane Mʼbatizi
Ndipo Yesu atamaliza kulangiza ophunzira ake khumi ndi awiri aja, anachoka kumeneko kupita kukaphunzitsa ndi kukalalikira ku mizinda ya ku Galileya.
Yohane ali mʼndende anamva zimene Khristu ankachita, ndipo anatumiza ophunzira ake kukamufunsa Iye. Anamufunsa kuti, “Kodi Inu ndinu uja ankanena kuti mudzabwerayu kapena tidikire wina?”
Yesu anayankha kuti, “Bwererani ndi kukamuwuza Yohane zimene mwamva ndi kuona. Osaona akuona, olumala akuyenda, akhate akuchiritsidwa, osamva akumva, akufa akuukitsidwa ndipo Uthenga Wabwino ukulalikidwa kwa osauka. Odala ndi munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”
Pamene ophunzira a Yohane ankachoka, Yesu anayamba kuyankhula kwa gulu la anthu za Yohane kuti, “Kodi munkapita ku chipululu kuti mukaone chiyani? Kodi bango logwedezeka ndi mphepo? Nanga munkapita kukaona chiyani, munthu wovala zokongola? Ayi, wovala zokongola amakhala mʼnyumba za mafumu. Nanga munkapita kukaona chiyani? Mneneri kodi? Inde ndikuwuzani kuti munkakaona woposa mneneri. 10  Uyu ndi amene malemba akunena za iye kuti,
“Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu
amene adzakonza njira yanu.
11  Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pakati pa obadwa ndi mkazi sipanaoneke wina aliyense wamkulu woposa Yohane Mʼbatizi; komatu amene ndi wamngʼono kwambiri mu ufumu wakumwamba ndi wamkulu koposa iye. 12  Kuyambira masiku a Yohane Mʼbatizi mpaka tsopano, ufumu wakumwamba ndi wolimbirana ndipo anthu amphamvu okha ndi amene akuwulanda. 13  Pakuti aneneri onse ndi malamulo ananenera kufikira nthawi ya Yohane. 14  Ndipo ngati inu mufuna kulandira izi, iyeyu ndi Eliya amene ankanena kuti adzabwera uja. 15  Iye amene ali ndi makutu amve.
16  “Kodi mʼbado uwu ndingawufanizire ndi chiyani? Uli ngati ana opezeka mʼmisika amene akuyitana anzawo nʼkumati:
17  “ ‘Tinakuyimbirani zitoliro,
koma inu simunavine;
ife tinayimba nyimbo zamaliro,
koma inu simunalire.’
18  Pakuti Yohane sanabwerere kudya kapena kumwa koma iwo ankanena kuti, ‘Iye anali ndi chiwanda.’ 19  Mwana wa Munthu anabwera ndi kumadya ndi kumwa koma iwo akuti, ‘Munthu wadyera, woledzera, bwenzi la amisonkho ndi bwenzi la ochimwa.’ Koma nzeru imatsimikizika kuti ndi yolondola mwa ntchito zake.”
Tsoka la Mizinda Itatu Yosatembenuka mtima
20 Pamenepo Yesu anayamba kudzudzula mizinda imene zodabwitsa zake zambiri zinachitikamo, chifukwa chakuti sinatembenuke mtima. 21  “Tsoka kwa iwe Korazini! Tsoka kwa iwe Betisaida! Ngati zodabwitsa zimene zinachitika mwa iwe zikanachitidwa mu Turo ndi Sidoni, iwo akanalapa kale atavala ziguduli ndi kudzola phulusa. 22  Koma ndikuwuzani inu kuti pa tsiku lachiweruzo mlandu wa Turo ndi Sidoni udzachepako kusiyana ndi wanu. 23  Ndipo iwe Kaperenawo, kodi udzakwezedwa kufika kumwamba? Ayi, udzatsitsidwa mpaka pansi kufika ku Hade. Ngati zodabwitsa zimene zinachitika mwa iwe, zikanachitika mu Sodomu, bwenzi iye alipo kufikira lero. 24  Koma Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro mlandu wa Sodomu udzachepako kusiyana ndi wanu.”
Goli la Khristu
25 Pa nthawi imeneyo Yesu anati, “Ine ndikukuyamikani Inu Atate Ambuye akumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa Inu mwawabisira zinthu izi anzeru ndi ophunzira ndi kuziwulula kwa ana angʼonoangʼono. 26  Inde, Atate, ichi chinali chokukomerani Inu.
27  “Zinthu zonse zapatsidwa kwa Ine ndi Atate anga. Palibe mmodzi amene adziwa Mwana kupatula Atate ndipo palibe mmodzi amene adziwa Atate kupatula Mwana ndi kwa iwo amene Mwana awasankha kuwawululira.
28  “Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. 29  Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. 30  Pakuti goli langa ndi losavuta ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”