18
Fanizo la Mayi Wakhama pa Kupempha
Kenaka Yesu anawuza ophunzira ake fanizo kuwaonetsa kuti iwo ayenera kumapemphera nthawi zonse ndikuti asafowoke. Iye anati, “Mʼmudzi wina munali woweruza wosaopa Mulungu ngakhalenso kulabadira za anthu. Ndipo panali mkazi wamasiye mʼmudzimo amene ankabwerabwera kwa iye ndi dandawulo lake kuti, ‘Mundiweruze mlandu mwachilungamo pakati pa ine ndi otsutsana nane.’
“Kwa nthawi yayitali woweruzayo ankakana. Koma pa mapeto analingalira nati, ‘Ngakhale kuti sindiopa Mulungu kapena kulabadira za anthu, koma chifukwa chakuti mkazi wamasiyeyu akundivutitsa, ine ndimuweruzira mlandu wake mwachilungamo kuti asanditopetse ndi kubwerabwera kwakeko!’ ”
Ndipo Ambuye anati, “Tamvani zimene woweruza wopanda chilungamoyu wanena. Tsono chingamuletse nʼchiyani Mulungu kubweretsa chilungamo kwa osankhika ake, amene amalira kwa Iye usana ndi usiku? Kodi adzapitirirabe osawalabadira? Ine ndikukuwuzani inu, adzaonetsetsa kuti alandire chilungamo, ndiponso mofulumira. Komabe, pamene Mwana wa Munthu akubwera, kodi adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi?”
Fanizo la Mfarisi ndi Wolandira Msonkho
Yesu ananena fanizoli kwa amene amadzikhulupirira mwa iwo okha kuti anali wolungama nanyoza ena onse. 10  “Anthu awiri anapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera, wina Mfarisi ndi winayo wolandira msonkho. 11  Mfarisiyo anayimirira ndipo anapemphera za iye mwini kuti, ‘Mulungu, ine ndikuyamika kuti sindili ngati anthu ena onse, achifwamba, ochita zoyipa, achigololo, sindilinso ngati wolandira msonkhoyu. 12  Ine ndimasala kudya kawiri pa Sabata ndipo ndimapereka chakhumi pa zonse ndimapeza.’
13  “Koma wolandira msonkhoyo ali chiyimire potero, sanathe nʼkomwe kuyangʼana kumwamba; koma anadziguguda pachifuwa ndipo anati, ‘Mulungu, chitireni chifundo, ine wochimwa.’
14  “Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”
Yesu Adalitsa Ana Aangʼono
15 Anthu amabweretsanso ana aangʼono kwa Yesu kuti awadalitse. Ophunzira ataona izi, anawadzudzula. 16 Koma Yesu anayitana anawo kuti abwere kwa Iye nati, “Lolani ana abwere kwa Ine ndipo musawatsekereze, pakuti ufumu wa Mulungu uli wa anthu otere. 17  Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene salandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamngʼono, sadzalowamo.”
Munthu Wachuma ndi Ufumu wa Mulungu
18 Oweruza wina wake anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?”
19 Yesu anamuyankha kuti, “Chifukwa chiyani ukunditcha wabwino, palibe wabwino kupatula Mulungu yekha. 20  Iwe umadziwa malamulo: ‘Usachite chigololo, usaphe, usabe, usapereke umboni wonama, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”
21 Iye anati, “Zonsezi ndinasunga kuyambira ndili mnyamata.”
22 Yesu atamva izi, anati kwa iye, “Ukusowabe chinthu chimodzi: Gulitsa zonse zimene uli nazo ndipo uzipereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Kenaka ubwere, nunditsate ine.”
23 Atamva zimenezi, anakhumudwa kwambiri chifukwa anali munthu wachuma chambiri. 24 Yesu anamuyangʼana nati, “Nʼkwapatali kwambiri kuti anthu achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu! 25  Ndithudi, nʼkwapafupi kuti ngamira idutse pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.”
26 Amene anamva izi anafunsa kuti, “Nanga ndani amene angapulumuke?”
27 Yesu anayankha kuti, “Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu.”
28 Petro anati kwa Iye, “Ife tinasiya zonse tinali nazo kutsatira Inu!”
29 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti palibe amene anasiya nyumba kapena mkazi kapena abale kapena makolo kapena ana chifukwa cha ufumu wa Mulungu 30  adzalephera kulandira mowirikiza mʼmoyo uno, ndi mʼmoyo ukubwerawo, moyo wosatha.”
Yesu Aneneratu za Imfa Yake Kachitatu
31 Yesu anatengera khumi ndi awiriwo pambali ndi kuwawuza kuti, “Taonani ife tikupita ku Yerusalemu, ndipo zonse zimene zalembedwa ndi Aneneri za Mwana wa Munthu zidzakwaniritsidwa. 32  Iye adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina. Ndipo adzamuchita chipongwe, adzamunyoza, adzamulavulira, 33  adzamukwapula ndi kumupha. Tsiku lachitatu Iye adzaukanso.”
34 Ophunzira sanazindikire china chilichonse cha izi. Tanthauzo lake linabisika kwa iwo, ndipo sanadziwe chimene Iye amayankhula.
Yesu Achiritsa Wosaona
35 Yesu atayandikira ku Yeriko, munthu wina wosaona amene amakhala pambali pa msewu namapempha, 36 anamva gulu la anthu likudutsa. Iye anafunsa chomwe chimachitika. 37 Iwo anamuwuza kuti “Yesu wa ku Nazareti akudutsa.”
38 Iye anayitana mofuwula, “Yesu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”
39 Iwo amene amamutsogolera njira anamudzudzula ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulabe, “Mwana wa Davide, chitireni chifundo!”
40 Yesu anayima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atabwera pafupi, Yesu anamufunsa kuti, 41  “Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?”
Iye anayankha kuti, “Ambuye, ine ndifuna ndionenso.”
42 Yesu anati kwa iye, “Onanso; chikhulupiriro chako chakupulumutsa.” 43 Nthawi yomweyo anaonanso ndipo anayamba kumutsatira Yesu, akulemekeza Mulungu. Anthu onse ataona izi, iwonso analemekeza Mulungu.