11
Davide ndi Batiseba
1 Nthawi ya mphukira, nthawi imene mafumu amapita ku nkhondo, Davide anatumiza Yowabu ndi ankhondo a mfumu pamodzi ndi gulu lonse lankhondo la Aisraeli. Iwo anawononga Aamoni ndi kuzungulira mzinda wa Raba. Koma Davide anatsala ku Yerusalemu.
2 Tsiku lina cha kumadzulo Davide anadzuka pa bedi lake ndipo ankayenda pamwamba pa nyumba yake. Ali pa dengapo anaona mkazi akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwambiri. 3 Ndipo Davide anatuma munthu wina kuti akafufuze za iye. Munthuyo anati, “Kodi uyu si Batiseba, mwana wa Eliamu, mkazi wa Uriya Mhiti?” 4 Ndipo Davide anatumiza amithenga kwa iye kukamuyitana. Batiseba anabwera kwa Davide ndipo anagona naye. (Nʼkuti mkaziyu atayeretsedwa ku masiku ake osamba). Kenaka anabwerera ku nyumba yake. 5 Mkaziyo anakhala woyembekezera ndipo anatumiza mawu kwa Davide kunena kuti, “Ine ndine woyembekezera.”
6 Ndipo Davide anatumiza mawu awa kwa Yowabu: “Nditumizire Uriya Mhiti.” Ndipo Yowabu anamutumiza kwa Davide. 7 Uriya atafika kwa Davide, Davide anamufunsa za momwe analili Yowabu, za asilikali ndi momwe nkhondo inkayendera. 8 Kenaka Davide anati kwa Uriya, “Pita ku nyumba yako ukapumule.” Choncho Uriya anachoka ku nyumba yaufumu, ndipo mfumuyo inatumiza mphatso kwa Uriya. 9 Koma Uriya anagona pa chipata cha nyumba yaufumu pamodzi ndi antchito onse a mbuye wake ndipo sanapite ku nyumba yake.
10 Davide atawuzidwa kuti, “Uriya sanapite ku nyumba yake.” Iye anafunsa kuti, “Kodi iwe sunachokera kutali? Nʼchifukwa chiyani sunapite ku nyumba yako?”
11 Uriya anayankha Davide kuti, “Bokosi la Chipangano ndi Israeli ndiponso Yuda akukhala mʼmatenti, ndipo mbuye wanga Yowabu ndi ankhondo anu mbuye wanga amanga misasa pa mtetete. Ine ndingapite bwanji ku nyumba yanga kukadya ndi kumwa ndiponso kugona ndi mkazi wanga? Pali inu wamoyo, ine sindidzachita chinthu chimenechi.”
12 Ndipo Davide anati kwa iye, “Ukhale konkuno tsiku lina limodzi, ndipo mawa ndikulola kuti upite.” Kotero Uriya anakhala mu Yerusalemu tsiku limenelo ndi tsiku linalo. 13 Davide anayitana Uriya nadya ndi kumwa naye, ndipo Davide anamuledzeretsa. Koma madzulo Uriya anapita kukagona pa mphasa pamodzi ndi antchito a mbuye wake. Iye sanapite ku nyumba yake.
14 Mmawa Davide analemba kalata kwa Yowabu ndipo anayitumiza ndi Uriya. 15 Mʼkalatayo analembamo kuti, “Uriya mumuyike patsogolo penipeni, pamene pali nkhondo yoopsa. Ndipo mumusiye yekha kuti akanthidwe ndi kufa.”
16 Kotero Yowabu atawuzinga mzindawo, anamuyika Uriya pamalo pamene amadziwa kuti pali asilikali amphamvu. 17 Ankhondo a mu mzindawo atabwera kudzamenyana ndi Yowabu, anthu ena a gulu la ankhondo la Davide anaphedwa ndipo Uriya Mhiti uja anaphedwanso.
18 Yowabu anatumiza wamthenga kwa Davide kukafotokoza mwatsatanetsatane za nkhondoyo. 19 Iye anamulangiza wa mthengayo kuti, “Pamene ukatsiriza kufotokozera mfumu za ku nkhondozi, 20 mfumu ikapsa mtima, ndipo akakakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani munapita pafupi ndi mzindawo kukamenya nkhondo? Inu simunadziwe kuti atha kukuponyerani mivi kuchokera pa khoma? 21 Kodi anapha Abimeleki mwana wa Yerubeseti ndani? Kodi mkazi sanamuponyere mphero kuchokera pa khoma? Kotero kuti anakafera ku Tebezi. Nʼchifukwa chiyani munafika pafupi ndi khoma?’ Ngati iye akafunsa zimenezi, iwe ukanene kwa iye kuti, ‘Mtumiki wanunso Uriya Mhiti wafa.’ ”
22 Mthengayo ananyamuka, ndipo atafika anamuwuza Davide zonse zimene Yowabu anamutuma kuti akanene. 23 Mthengayo anati kwa Davide, “Anthuwo anatiposa mphamvu ndipo anabwera kudzalimbana nafe poyera, koma ife tinawabwezera ku chipata cha mzindawo. 24 Ndipo anthu oponya mivi anatiponyera kuchokera pa khoma, anthu ena a mfumu afa. Kuwonjezera apo, mtumiki wanu Uriya Mhiti wafanso.”
25 Davide anamuwuza mthengayo kuti, “Ukanene izi kwa Yowabu: ‘Zimenezi zisakukhumudwitse; lupanga limapha wina nthawi zinanso wina. Limbikitsa nkhondo pa mzindawo ndipo uwuwononge!’ Ukanene zimenezi pomulimbikitsa Yowabu.”
26 Mkazi wa Uriya atamva kuti mwamuna wake wafa, analira maliro. 27 Nthawi yolira maliro itatha, Davide anamubweretsa ku nyumba yake, ndipo anakhala mkazi wake nabala mwana wamwamuna. Koma Yehova sanakondwe ndi zimene Davide anachitazo.