2
Kuweruza Kolungama kwa Mulungu
Choncho, iwe amene umaweruza munthu wina, ulibe pokanira pakuti nthawi iliyonse pamene uweruza wina ukudzitsutsa wekha chifukwa iwe amene umaweruzawe umachitanso zinthu zomwezo. Tsopano ife tikudziwa kuti chiweruzo cha Mulungu, chotsutsa amene amachita zinthu zotere, nʼchokhazikika pa choonadi. Kodi ukuganiza kuti udzathawa chiweruzo cha Mulungu iwe munthu wamba, pamene uweruza ena, iwe ndi kumachitanso zomwezo? Kodi kapena ukupeputsa kukoma mtima kwa Mulungu, kuleza mtima kwake ndi kupirira kwake? Kodi sukuzindikira kuti kukoma mtima kwakeko, nʼkofuna kuti iweyo ulape machimo ako?
Koma pakuti ndiwe wosamvera ndi wa mtima wosafuna kulapa, ukudzisungira chilango pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu, pamene chiweruzo cholungama cha Mulungu chidzaonetsedwa. Mulungu adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake. Iye adzapereka moyo wosatha kwa amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pochita ntchito zabwino mopirira. Koma Mulungu adzakhuthulira mkwiyo ndi ukali wake pa amene amachita zofuna zawo ndi kukana choonadi nʼkumatsatira zoyipa. Masautso ndi zowawa zidzagwera munthu aliyense amene amachita zonyansa, kuyambira Myuda kenaka anthu a mitundu ina. 10 Koma ulemerero, ulemu ndi mtendere zidzakhala kwa aliyense amene amachita zabwino, kuyambira Myuda kenaka anthu a mitundu ina. 11 Pajatu Mulungu alibe tsankho.
12 Onse amene amachimwa osadziwa Malamulo, adzawonongeka ngakhale kuti sadziwa Malamulowo. Ndipo onse amene amachimwa akudziwa Malamulo adzaweruzidwa potsata Malamulowo. 13 Pakuti si amene amangomva Malamulo amene amakhala wolungama pamaso pa Mulungu, koma ndi okhawo amene amachita zili mʼMalamulomo amene adzatchedwa olungama. 14 Ndithu, pamene a mitundu ina, amene alibe Malamulo, koma mwachikhalidwe chawo amachita zimene zili mʼMalamulo, iwowo ndi Malamulo pa iwo okha, ngakhale kuti alibe Malamulowo. 15 Ntchito zawo zimaonetsa kuti Malamulowo alembedwa mʼmitima mwawo. Chikumbumtima chawonso chimawachitira umboni pakuti maganizo awo amawatsutsa kapena kuwavomereza. 16 Izi zidzachitika pa tsiku limene Mulungu adzaweruza zinsinsi za anthu kudzera mwa Yesu Khristu, monga momwe Uthenga wanga Wabwino unenera.
Ayuda ndi Malamulo
17 Koma iweyo, amene umadzitcha kuti ndiwe Myuda, umadalira Malamulo, ndipo umanyadira ubale wako ndi Mulungu, 18 ngati umadziwa chifuniro chake, ndi kudziwa zoyenera kuchita chifukwa unaphunzitsidwa ndi Malamulo; 19 ngati umadziwadi kuti ndiwe mtsogoleri wa osaona, nyale yowunikira amene ali mu mdima, 20 mlangizi wa anthu opusa, mphunzitsi wa makanda, chifukwa umadziwa kuti mʼMalamulo uli nayo nzeru yonse ndi choonadi, 21 tsono, iwe amene umaphunzitsa ena, sudziphunzitsa wekha kodi? Kodi iwe amene umalalikira kuti anthu asabe, umabanso? 22 Kodi iwe amene umanena kuti anthu asachite chigololo, umachitanso chigololo? Kodi iwe amene umanyasidwa ndi mafano, umalandanso za mʼnyumba zopembedzera mafanowo? 23 Kodi iwe amene umadzitama ndi Malamulo, umamuchititsa manyazi Mulungu posamvera Malamulowo? 24 Monga kwalembedwa, “Dzina la Mulungu likuchitidwa chipongwe pakati pa a mitundu ina chifukwa cha inu.”
25 Mdulidwe umakhala ndi phindu ngati usunga Malamulo, koma ngati sumvera Malamulo, iweyo umakhala ngati kuti sunachite mdulidwe. 26 Ngati amene sanachite mdulidwe achita zomwe zili mʼMalamulo, kodi sadzatengedwa ngati ochita mdulidwe? 27 Munthu amene sanachite mdulidwe mʼthupi koma amamvera Malamulo adzakutsutsa iwe wosamvera Malamulowe, ngakhale kuti uli nawo Malamulo olembedwawo.
28 Myuda weniweni si amene angooneka ngati Myuda pamaso pa anthu, ndipo mdulidwe weniweni si umene umangochitika mʼthupi pamaso pa anthu. 29 Ayi, Myuda weniweni ndi amene ali Myuda mu mtima mwake, ndipo mdulidwe weniweni ndi wa mtima, wochitika ndi Mzimu, osati ndi malamulo olembedwa. Woyamikira munthu wotere ndi Mulungu, osati anthu ayi.