Salimo 105
1 Yamikani Yehova, itanani dzina lake;
lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.
2 Imbirani Iye, imbani matamando kwa Iyeyo;
fotokozani za machitidwe ake onse odabwitsa.
3 Munyadire dzina lake loyera;
mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere.
4 Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;
funafunani nkhope yake nthawi yonse.
5 Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita,
zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka,
6 inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,
inu ana a Yakobo, osankhika ake.
7 Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;
maweruzo ake ali pa dziko lonse lapansi.
8 Iyeyo amakumbukira pangano lake kwamuyaya,
mawu amene analamula kwa mibado yonse,
9 pangano limene Iye anapanga ndi Abrahamu,
lumbiro limene analumbira kwa Isake.
10 Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga zophunzitsa,
kwa Israeli monga pangano lamuyaya:
11 “Ndidzapereka kwa iwe dziko la Kanaani
ngati gawo la cholowa chako.”
12 Pamene iwo anali ngati anthu ochepa mʼchiwerengero,
ochepa ndithu, ndiponso alendo mʼdzikolo,
13 ankayendayenda kuchoka ku mtundu wina wa anthu ndi kupita ku mtundu wina,
kuchoka mu ufumu wina kupita ku wina.
14 Iye sanalole wina aliyense kuwapondereza;
anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo:
15 “Musakhudze odzozedwa anga;
musachitire choyipa aneneri anga.”
16 Iye anabweretsa njala pa dziko
ndipo anawononga chakudya chonse;
17 Iyeyo anatumiza munthu patsogolo pawo,
Yosefe anagulitsidwa ngati kapolo.
18 Iwo anavulaza mapazi ake ndi matangadza,
khosi lake analiyika mʼzitsulo,
19 mpaka zimene Iye ananeneratu zitakwaniritsidwa,
mpaka mawu a Yehova ataonetsa kuti Iye ananena zoona.
20 Mfumu inatuma munthu kukamumasula,
wolamulira wa mitundu ya anthu anamasula iyeyo.
21 Anamuyika kukhala wolamulira nyumba yake,
wolamulira zonse zimene iye anali nazo,
22 kulangiza ana a mfumu monga ankafunira
ndi kuphunzitsa nzeru akuluakulu.
23 Tsono Israeli analowa mu Igupto;
Yakobo anakhala monga mlendo mʼdziko la Hamu.
24 Yehova anachulukitsa anthu ake;
ndipo anachititsa kuti akhale ochuluka kwambiri kuposa adani awo;
25 amene mitima yawo anayitembenuza kuti idane ndi anthu ake,
kukonzera chiwembu atumiki ake.
26 Yehova anatuma Mose mtumiki wake,
ndi Aaroni amene Iye anamusankha.
27 Iwo anachita zizindikiro zozizwitsa pakati pawo,
zodabwitsa zake mʼdziko la Hamu.
28 Yehova anatumiza mdima nasandutsa dziko kuti likhale la mdima.
Koma anthuwo anakaniratu mawu a Yehova.
29 Yehova anasandutsa madzi awo kukhala magazi,
kuchititsa kuti nsomba zawo zife.
30 Dziko lawo linadzaza ndi achule
amene analowa mʼzipinda zogona za olamulira awo.
31 Iye anayankhula, ndipo kunabwera ntchentche zochuluka
ndi nsabwe mʼdziko lawo lonse.
32 Iyeyo anatembenuza mvula yawo kukhala matalala,
ndi zingʼaningʼani mʼdziko lawo lonse;
33 Anagwetsa mitengo yawo ya mpesa ndi mitengo yawo ya mkuyu,
nawononganso mitengo ina ya mʼdziko lawolo.
34 Iye anayankhula, ndipo dzombe linabwera,
ziwala zosawerengeka;
35 zinadya chilichonse chobiriwira cha mʼdziko lawo,
zinadya zonse zotuluka mʼnthaka yawo.
36 Kenaka anakantha ana onse oyamba kubadwa a mʼdziko lawo,
zipatso zoyamba za umunthu wawo wonse.
37 Yehova anatulutsa Israeli, atatenga siliva ndi golide wambiri,
ndipo pakati pa mafuko awo palibe mmodzi amene anafowoka.
38 Dziko la Igupto linakondwa pamene iwo anachoka,
pakuti kuopsa kwa Israeli kunawagwera iwo.
39 Iye anatambasula mitambo ngati chofunda chawo,
ndi moto owawunikira usiku.
40 Iwo anapempha, ndipo Iye anawabweretsera zinziri
ndipo anawakhutitsa ndi chakudya chochokera kumwamba.
41 Iye anatsekula thanthwe, ndipo madzi anatuluka;
ngati mtsinje anayenda mʼchipululu.
42 Pakuti anakumbukira lonjezo lake loyera limene
linaperekedwa kwa Abrahamu mtumiki wake.
43 Iye anatulutsa anthu ake akukondwera,
osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;
44 Iye anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina
ndipo anakhala olowamʼmalo a zimene ena anazivutikira,
45 kuti iwo asunge malangizo ake
ndi kutsatira malamulo ake.
Tamandani Yehova.