3
Osakhulupirira za Thupi
1 Abale anga, ndikupitiriza kunena kuti, kondwani mwa Ambuye! Sizondivuta kuti ndilembenso mawu omwewo, ndipo zimenezi nʼzokuthandizani inuyo.
2 Chenjerani ndi agalu amenewa, anthu ochita zoyipa, anthu amene amadula thupi lawo. 3 Pakuti ochita mdulidwe weniweni ndife. Ife amene timatumikira Mulungu motsogozedwa ndi Mzimu. Ife amene timanyadira Khristu, ndipo sitidalira zinthu za thupi 4 ngakhale kuti ineyo ndili ndi zifukwa zokwanira kudalira zinthu za thupizo.
Ngati pali winanso amene akuganiza kuti ali ndi zifukwa zokwanira kudalira zinthu za thupi, ineyo ndili ndi zifukwa zoposa pamenepo. 5 Ndinachita mdulidwe pa tsiku lachisanu ndi chitatu nditangobadwa. Ndine wa mtundu wa Israeli, wa fuko la Benjamini, Mhebri wa Ahebri, kunena za malamulo, ndinali Mfarisi. 6 Kunena za changu changa, ndinkazunza mpingo. Kunena za chilungamo chopezeka chifukwa chotsata malamulo, ineyo ndinali wopanda cholakwa.
7 Koma zonse zimene ndinkaziyesa zaphindu, tsopano ndikuziona kuti nʼzosapindulitsa chifukwa cha Khristu. 8 Kuwonjeza pamenepo, ndikuziona zonse kuti nʼzopanda phindu poyerekeza ndi phindu lopambana la kudziwa Khristu Yesu Ambuye anga. Nʼchifukwa cha Yesuyo ndataya zinthu zonse ndipo ndikuziyesa zinyalala kuti ndipindule Khristu 9 ndi kuti ndipezeke mwa Iyeyo, osati ndi chilungamo changa chobwera chifukwa chotsata malamulo, koma chimene chimabwera chifukwa chokhulupirira Khristu. Chilungamochi nʼchochokera kwa Mulungu, timachilandira mwachikhulupiriro. 10 Ine ndikufuna kudziwa Khristu, ndithu, kudziwa mphamvu zake za kuuka kwa akufa. Ndikufuna kuyanjana naye mʼmasautso ake, kufanana naye pa imfa yake 11 kuti nanenso ndidzaukitsidwe kwa akufa.
Kuthamanga Mpaka Kumapeto pa Mpikisano wa Liwiro
12 Sikuti ndazipeza kale zonsezi, kapena kuti ndakhala kale wangwiro, koma ndikuthamangabe ndi kuyesetsa kuti ndipeze chimene Khristu Yesu anandiyitanira. 13 Abale, sindidziyesera ndekha kuti ndachipeza kale chimenechi. Koma chinthu chimodzi chimene ndimachita, nʼkuyiwala zamʼmbuyo ndi kuthamangira molimbika zinthu zimene zili mʼtsogolo mwanga. 14 Ndikuthamangira kokathera mpikisanowo kuti ndikalandire mphotho imeneyi kumwamba, imene Mulungu anandiyitanira mwa Khristu Yesu.
Kutsanzira Paulo
15 Choncho ife tonse amene tili okhwima pa moyo wauzimu, tikhale ndi maganizo omwewa. Ndipo ngati pena ndi pena muli ndi maganizo osiyana ndi amenewa, pameneponso Mulungu adzakuwunikirani. 16 Tiyeni ife tizikhala mogwirizana ndi zimene tinapeza kale basi.
17 Abale, nonsenu pamodzi mudzinditsanzira ine, ndipo monga inu muli ndi chitsanzo, phunzirani kwa amene akukhala moyo motsatira momwe timakhalira. 18 Pakuti monga ndakhala ndikukuwuzani kawirikawiri mʼmbuyomu, ndipo tsopano ndikunenanso ndi misozi kuti, anthu ambiri akukhala monga adani a mtanda wa Khristu. 19 Mapeto awo ndi chiwonongeko, mulungu wawo ndi mimba zawo, ndipo ulemerero wawo ndi manyazi awo. Mtima wawo uli pa zinthu za dziko lapansi. 20 Koma ife ndife nzika za kumwamba ndipo tikudikirira mwachidwi Mpulumutsi wochokera kumeneko, Ambuye Yesu Khristu. 21 Iyeyo, ndi mphamvu imene imamuthandiza kukhazikitsa zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, adzasintha matupi athu achabewa kuti akhale ofanana ndi thupi lake la ulemerero.