41
Mulungu Thandizo la Israeli
“Khalani chete pamaso panga, inu mayiko a mʼmbali mwa nyanja!
Alekeni ayandikire ndi kuyankhula;
tiyeni tikhale pamodzi
kuti atiweruze.
 
“Ndani anadzutsa wochokera kummawa
uja amene ananka napambana kulikonse kumene ankapita?
Iye amapereka anthu a mitundu ina mʼmanja mwake
ndipo ndi lupanga lake anagonjetsa
ndi kusandutsa mafumu kukhala ngati fumbi
nawamwaza ngati mankhusu ndi uta wake.
Amawalondola namayenda mosavutika,
mʼnjira imene mapazi ake sanayendemo kale.
Ndani anachita zimenezi ndi kuzitsiriza,
si uja amene anayambitsa mitundu ya anthu?
Ine Yehova, ndine chiyambi
ndipo potsiriza pake ndidzakhalapo.”
 
Mayiko amʼmbali mwa nyanja aona zimenezi ndipo akuopa;
anthu a ku mathero a dziko lapansi akunjenjemera.
Akuyandikira pafupi, akubwera;
aliyense akuthandiza mnzake
ndipo akuwuza mʼbale wake kuti, “Limba mtima!”
Mʼmisiri wa matabwa amalimbikitsa mʼmisiri wa golide,
ndipo iye amene amasalaza fano ndi nyundo
amalimbikitsa amene amalisanja pa chipala.
Ponena za kuwotcherera iye amati, “Zili bwino.”
Iye amalikhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwe.
 
“Koma Iwe Israeli mtumiki wanga,
Yakobo amene ndakusankha,
Ndiwe chidzukulu cha Abrahamu bwenzi langa.
Ndinakutengani kuchokera ku mapeto a dziko lapansi,
ndinakuyitanani kuchokera ku mbali za kutali za dziko lapansi.
Ine ndinati, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga;’
Ndinakusankha ndipo sindinakutaye.
10 Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe;
usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako.
Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza,
ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
 
11 “Onse amene akupsera mtima
adzachita manyazi ndithu ndi kunyazitsidwa;
onse amene akukangana nawe
sadzakhalanso kanthu, adzawonongeka.
12 Udzafunafuna adani ako,
koma sadzapezeka.
Iwo amene akuchita nawe nkhondo
sadzakhalanso kanthu.
13 Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako,
amene ndikukugwira dzanja lako lamanja
ndipo ndikuti, usaope;
ndidzakuthandiza.
14 Usachite mantha, iwe Yakobo wofowoka ngati nyongolotsi,
iwe wochepa mphamvu Israeli,
chifukwa Ine ndidzakuthandiza,”
akutero Yehova Mpulumutsi wako, Woyerayo wa Israeli.
15 “Taona, ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tirigu
chatsopano, chakunthwa ndi cha mano ambiri.
Udzanyenya mapiri ndi kuwaphwanyaphwanya,
ndipo zitunda adzazisandutsa ngati mankhusu.
16 Udzawapeta ndipo adzawuluka ndi mphepo komanso
adzamwazika ndi kamvuluvulu.
Koma iwe udzakondwera chifukwa Ine ndine Mulungu wako,
ndipo udzanyadira chifukwa cha Ine Woyerayo wa Israeli:
 
17 “Pamene amphawi ndi osauka akufunafuna madzi,
koma sakuwapeza;
ndipo kummero kwawo kwawuma ndi ludzu.
Ine Yehova ndidzayankha pemphero lawo;
Ine, Mulungu wa Israeli, sindidzawasiya.
18 Ndidzayendetsa mitsinje mʼmalo owuma,
ndi akasupe adzatumphuka mu zigwa.
Ndidzasandutsa chipululu kukhala dziwe la madzi
ndipo dziko lowuma kukhala akasupe a madzi.
19 Mʼchipululu ndidzameretsa
mkungudza, kasiya mchisu ndi mtengo wa Olivi.
Mʼdziko lowuma ndidzaza mitengo
ya payini, ya mkuyu ndi ya mlombwa,
20 kuti anthu aone ndi kudziwa;
inde, alingalire ndi kumvetsa,
kuti Yehova ndiye wachita zimenezi;
kuti Woyera wa Israeli ndiye anakonza zimenezi.
 
21 “Yehova akuwuza milungu ina kuti, ‘Fotokozani mlandu wanu.’
Mfumu ya Yakobo ikuti, ‘Perekani umboni wanu.’
22 Bwerani ndi milungu yanu kuti idzatiwuze
zomwe zidzachitike mʼtsogolo.
Tifotokozereni zinthu zamakedzana
tiziganizire
ndi kudziwa zotsatira zake.
Kapena tiwuzeni zimene zidzachitike mʼtsogolo,
23 tiwuzeni kuti kutsogolo kuli zotani,
ndipo ife tidziwa kuti ndinu milungu.
Chitani chinthu chabwino kapena choyipa,
ndipo mutidabwitsa ndi kutichititsa mantha.
24 Koma inu sindinu kanthu
ndipo zochita zanu nʼzopandapake;
amene amapembedza inu ali ngati chinthu chokanidwa chifukwa ndi choyipa.
 
25 “Ndinawutsa munthu wina kumpoto ndipo anabwera,
munthu wochokera kummawa amene ndinamuyitana.
Amapondaponda olamulira ngati matope,
ngati ndi wowumba mbiya amene akuponda dongo.
26 Ndani anawululiratu zimenezi poyamba pomwe, kuti ife tidziwe,
kapena kutiwuziratu zisanachitike kuti ife tinene kuti, ‘Analondola?’
Palibe amene ananena,
palibe analengeza zimenezi,
palibe anamva mawu anu.
27 Ine ndinali woyamba kumuwuza Ziyoni kuti, ‘Taona, si awa akubwera apawa!’
Ndinatumiza mthenga wa nkhani yabwino ku Yerusalemu.
28 Koma ndikayangʼana palibe ndi mmodzi yemwe,
palibe ndi mmodzi yemwe pakati pawo wotha kupereka uphungu,
palibe woti ayankhe pamene ine ndawafunsa.
29 Taonani, milungu yonseyi ndi yachinyengo!
Zochita zawo si kanthu konse;
mafano awo ali ngati mphepo yachabechabe.