2
Sonkhanani pamodzi, sonkhanani pamodzi,
inu mtundu wochititsa manyazi,
isanafike nthawi yachiweruzo,
nthawi yanu isanawuluke ngati mungu,
usanakufikeni mkwiyo woopsa wa Yehova,
tsiku la ukali wa Yehova lisanafike pa inu.
Funafunani Yehova, inu nonse odzichepetsa a mʼdziko,
inu amene mumachita zimene amakulamulani.
Funafunani chilungamo, funafunani kudzichepetsa;
mwina mudzatetezedwa
pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.
Za Afilisti
Gaza adzasiyidwa
ndipo Asikeloni adzasanduka bwinja.
Nthawi yamasana Asidodi adzakhala wopanda anthu
ndipo Ekroni adzazulidwa.
Tsoka inu okhala mʼmbali mwa nyanja,
inu mtundu wa Akereti;
mawu a Yehova akutsutsa
iwe Kanaani, dziko la Afilisti.
“Ndidzakuwononga
ndipo palibe amene adzatsale.”
 
Dziko la mʼmbali mwa nyanja, kumene kumakhala Akereti,
lidzakhala malo a abusa ndi la makola a nkhosa.
Malowa adzakhala a anthu otsala a nyumba ya Yuda;
adzapezako msipu.
Nthawi ya madzulo adzagona
mʼnyumba za Asikeloni.
Yehova Mulungu wawo adzawasamalira;
adzabwezeretsa mtendere wawo.
Za Mowabu ndi Amoni
“Ndamva kunyoza kwa Mowabu
ndi chipongwe cha Amoni,
amene ananyoza anthu anga
ndi kuopseza kuti alanda dziko lawo.
Choncho, pali Ine Wamoyo,”
akutero Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli,
“Ndithu, Mowabu adzasanduka ngati Sodomu,
Amoni adzasanduka ngati Gomora;
malo a zomeramera ndi maenje a mchere,
dziko la bwinja mpaka muyaya.
Anthu anga otsala adzawafunkha;
opulumuka a mtundu wanga adzalandira dziko lawo.”
 
10 Ichi ndi chimene adzalandire chifukwa cha kunyada kwawo,
chifukwa chonyoza ndi kuchitira chipongwe anthu a Yehova Wamphamvuzonse.
11 Yehova adzawachititsa mantha kwambiri
pamene adzawononga milungu yonse ya mʼdzikomo.
Ndipo mitundu ya anthu pa dziko lonse idzamulambira,
uliwonse ku dziko la kwawo.
Za Kusi
12 “Inunso anthu a ku Kusi,
mudzaphedwa ndi lupanga.”
Za Asiriya
13 Yehova adzatambasulira dzanja lake kumpoto
ndi kuwononga Asiriya,
kusiya Ninive atawonongekeratu
ndi owuma ngati chipululu.
14 Nkhosa ndi ngʼombe zidzagona pansi kumeneko,
pamodzi ndi nyama zakuthengo za mtundu uliwonse.
Akadzidzi a mʼchipululu ndi akanungu
adzakhala pa nsanamira zake.
Kulira kwawo kudzamveka mʼmazenera,
mʼmakomo mwawo mudzakhala zinyalala zokhazokha,
nsanamira za mkungudza zidzakhala poonekera.
15 Umenewu ndiye mzinda wosasamala
umene kale unali wotetezedwa.
Unkanena kuti mu mtima mwake,
“Ine ndine, ndipo palibenso wina wondiposa.”
Taonani lero wasanduka bwinja,
kokhala nyama zakutchire!
Onse owudutsa akuwunyoza
ndi kupukusa mitu yawo.