42
Yobu
1 Pamenepo Yobu anayankha Yehova kuti,
2 “Ndikudziwa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse;
chimene mufuna kuchita wina sangaletse konse.
3 Munandifunsa kuti, ‘Kodi ndiwe yani amene ukufuna kusokoneza uphungu wanga ndi mawu opanda nzeru?
Zoonadi ndinayankhula zimene sindinazimvetse,
zinthu zodabwitsa kwambiri kwa ine zimene sindinazidziwe.
4 “Inu munandiwuza kuti, ‘Mvetsetsa tsopano ndipo ndidzayankhula;
ndidzakufunsa
ndipo iwe udzandiyankhe.’
5 Ndinkangomva za Inu ndi makutu anga,
koma tsopanonso ndakuonani ndi maso anga.
6 Nʼchifukwa chake ndi kuchita manyazi,
ndikulapa podzithira fumbi ndi phulusa.”
Mulungu Adalitsa Yobu
7 Yehova atayankhula ndi Yobu mawu amenewa anawuza Elifazi wa ku Temani kuti, “Ine ndakukwiyira pamodzi ndi abwenzi ako awiri, chifukwa simunayankhule zabwino za Ine, monga mmene wayankhulira mtumiki wanga Yobu. 8 Kotero tsopano mutenge ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi kupita nazo kwa mtumiki wanga Yobu kuti mukapereke nsembe zopsereza. Mtumiki wanga Yobu adzakupemphererani, ndipo Ine ndidzalandira pemphero lake. Sindidzakuchitirani kanthu molingana ndi uchitsiru wanu. Inu simunayankhule zabwino za Ine, monga anayankhulira Yobu mtumiki wanga.” 9 Motero Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki ndi Zofari wa ku Naama anachita zimene Yehova anawawuza ndipo Yehova anamvera pemphero la Yobu.
10 Yobu atawapempherera abwenzi ake aja, Yehova anamubwezera chuma chake ndipo anamupatsa mowirikiza kuposa zomwe anali nazo kale. 11 Abale ake ndi alongo ake onse, kuphatikizapo onse amene ankamudziwa kale, amabwera kwa iye nʼkudzadya naye chakudya mʼnyumba mwake. Iwo anamutonthoza ndi kumupepesa chifukwa cha mavuto onse amene Yehova analola kuti amugwere. Aliyense wa iwowa anamupatsa ndalama ndi mphete yagolide.
12 Yehova anadalitsa Yobu pa masiku ake otsirizawa kupambana poyamba paja. Iye anali ndi nkhosa 14,000, ngamira 6,000, ngʼombe zantchito 2,000 ndi abulu aakazi 1,000. 13 Anaberekanso ana aamuna asanu ndi awiri ndi ana aakazi atatu. 14 Mwana wake wamkazi woyamba anamutcha Yemima, wachiwiri anamutcha Keziya, wachitatu anamutcha Kereni Hapuki. 15 Mʼdziko monsemo munalibe akazi okongola ngati ana a Yobu, ndipo abambo awo anawapatsa cholowa pamodzi ndi alongo awo.
16 Zitachitika zimenezi, Yobu anakhala ndi moyo zaka 140. Iye anaona zidzukulu zake mpaka mʼbado wachinayi. 17 Potsiriza, Yobu anamwalira ali nkhalamba ya zaka zochuluka kwambiri.