9
Mawu a Yobu
Ndipo Yobu anayankha kuti,
“Zoonadi, ndikudziwa kuti zimenezi ndi zoona.
Koma munthu angathe bwanji kukhala wolungama pamaso pa Mulungu?
Ngakhale wina atafuna kutsutsana naye,
Iye sangamuyankhe munthuyo ngakhale mawu amodzi omwe.
Mulungu ndi wa nzeru zambiri ndipo mphamvu zake ndi zochuluka.
Ndani analimbana naye popanda kupwetekeka?
Iye amasuntha mapiri, mapiriwo osadziwa,
ndipo amawagubuduza ali wokwiya.
Iye amagwedeza dziko lapansi kulisuntha pamalo pake
ndipo amanjenjemeretsa mizati yake.
Iye amayankhula ndi dzuwa ndipo siliwala;
Iyeyo amaphimba kuwala kwa nyenyezi.
Ndi Mulungu yekha amene anayala mayiko akumwamba
ndipo amayenda pa mafunde a pa nyanja.
Iye ndiye mlengi wa nyenyezi zamlalangʼamba ndi akamwiniatsatana,
nsangwe ndi kumpotosimpita.
10 Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka,
zodabwitsa zimene sizingawerengeke.
11 Akapita pafupi ndi ine sindingathe kumuona;
akadutsa, sindingathe kumuzindikira.
12 Ngati Iye alanda zinthu, ndani angathe kumuletsa?
Ndani anganene kwa Iye kuti, ‘Mukuchita chiyani?’
13 Mulungu sabweza mkwiyo wake;
ngakhale gulu lankhondo la Rahabe linawerama pa mapazi ake.
 
14 “Nanga ine ndingathe kukangana naye bwanji?
Ndingawapeze kuti mawu oti nʼkutsutsana naye?
15 Ngakhale nditakhala wosalakwa, sindingamuyankhe;
ndikanangopempha chifundo kwa woweruza wanga.
16 Ngakhale ndikanamuyitana ndipo Iye ndi kuvomera,
sindikhulupirira kuti akanamva mawu angawo.
17 Iye akanandikantha ndi mphepo yamkuntho,
ndipo akanandipweteka popanda chifukwa.
18 Mulungu sakanandilola kuti ndipumenso
koma akanandichulukitsira zowawa.
19 Tikanena za mphamvu, Iye ndi wamphamvudi!
Ndipo tikanena za chiweruzo cholungama, ndani angamuzenge mlandu?
20 Ngakhale ndikanakhala wosalakwa, zoyankhula zanga zikananditsutsa;
ndikanakhala wopanda cholakwa, pakamwa panga pakanandipeza wolakwa.
 
21 “Ngakhale ine ndili wosalakwa,
sindidziyenereza ndekha;
moyo wanga ndimawupeputsa.
22 Zonse nʼzofanana; nʼchifukwa chake ndikuti,
‘Iye amawononga anthu osalakwa ndi anthu oyipa omwe.’
23 Pamene mkwapulo ubweretsa imfa yadzidzidzi,
Iye amaseka tsoka la munthu wosalakwayo.
24 Pamene dziko lagwa mʼmanja mwa anthu oyipa
Iye amawatseka maso anthu oweruza dzikolo.
Ngati si Iyeyo, nanga ndani?
 
25 “Masiku anga ndi othamanga kwambiri kupambana munthu waliwiro;
masikuwo amapita ine osaonapo zabwino.
26 Amayenda ngati mabwato a njedza pa nyanja,
ngati mphungu zothamangira nyama zoti zidye.
27 Nʼtanena kuti, ‘Ndidzayiwala madandawulo anga,
ndidzasintha nkhope yanga ndipo ndidzasekerera,’
28 ndikuopabe mavuto anga onse,
popeza ndikudziwa kuti simudzavomereza kuti ndine wosalakwa.
29 Popeza ndapezeka kale wolakwa
ndivutikirenji popanda phindu?
30 Ngakhale nditasamba mʼmadzi oyera kwambiri
ndi kusamba mʼmanja mwanga ndi sopo,
31 mutha kundiponyabe pa dzala,
kotero kuti ngakhale zovala zanga zomwe zidzandinyansa.
 
32 “Mulungu si munthu ngati ine kuti ndithe kumuyankha,
sindingathe kutsutsana naye mʼbwalo la milandu.
33 Pakanapezeka munthu wina kuti akhale mʼkhalapakati wathu,
kuti atibweretse ife tonse pamodzi,
34 munthu wina woti achotse ndodo ya Mulungu pa ine
kuti kuopsa kwake kusandichititsenso mantha!
35 Pamenepo ine ndikanatha kuyankhula mosamuopa Mulunguyo,
koma monga zililimu, sindingathe.