31
“Pa nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “Ndidzakhala Mulungu wa mafuko onse a Israeli, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”
Yehova akuti,
“Anthu amene anapulumuka ku nkhondo
ndinawakomera mtima mʼchipululu;
pamene Aisraeli ankafuna kupumula.”
Ine ndinawaonekera ndili chapatali ndipo ndinati,
“Ine ndakukondani ndi chikondi chopanda malire.
Nʼchifukwa chake ndipitiriza kukukondani.
Ndidzakusamaliraninso, inu anthu a Israeli;
mudzasangalala poyimba tizitoliro tanu,
ndipo mudzapita kukavina nawo
anthu ovina mwachimwemwe.
Mudzalimanso minda ya mpesa
pa mapiri a Samariya;
alimi adzadzala mphesa
ndipo adzadya zipatso zake.
Lidzafika tsiku pamene alonda adzafuwula
pa mapiri a Efereimu nati,
‘Tiyeni tipite ku Ziyoni,
kwa Yehova Mulungu wathu.’ ”
Yehova akuti,
“Imbani mosangalala chifukwa cha Yakobo,
fuwulani chifukwa cha mtundu wopambana mitundu yonse.
Matamando anu amveke, ndipo munene kuti,
‘Yehova wapulumutsa anthu ake
otsala a Israeli.’
Taonani, ndidzabwera nawo kuchokera ku dziko la kumpoto,
ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.
Anthu osaona, olumala, amayi oyembekezera
ndi amene ali pa nthawi yawo yochira adzabwera nawo pamodzi.
Chidzakhala chikhamu cha anthu obwerera kuno.
Adzabwera akulira;
koma Ine ndikuwatonthoza mtima, ndidzawaperekeza.
Ndidzawatsogolera ku mitsinje yamadzi
mʼnjira yosalala mmene sadzapunthwamo.
Chifukwa ndine abambo ake a Israeli,
ndipo Efereimu ndi mwana wanga woyamba.
 
10 “Imvani mawu a Yehova inu anthu a mitundu ina;
lalikirani mawuwa kwa anthu a mayiko akutali a mʼmbali mwa nyanja;
‘Iye amene anabalalitsa Israeli adzawasonkhanitsanso
ndipo adzayangʼanira nkhosa zake ngati mʼbusa.’
11 Pakuti Yehova wawombola fuko la Yakobo
anawapulumutsa mʼdzanja la anthu owaposa mphamvu.
12 Anthuwo adzabwera akuyimba mofuwula pa mapiri a Ziyoni;
adzasangalala ndi zinthu zabwino zochokera kwa Yehova.
Zinthu zabwinozo ndi izi: tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta,
ana ankhosa ndi ana angʼombe.
Iwo adzakhala ngati munda wothiriridwa bwino,
ndipo sadzamvanso chisoni.
13 Pamenepo anamwali adzavina ndi kusangalala.
Anyamata ndi okalamba nawonso adzasangalala.
Kulira kwawo ndidzakusandutsa chisangalalo;
ndidzawasangalatsa nʼkuchotsa chisoni chawo.
14 Ansembe ndidzawadyetsa chakudya chabwino,
ndipo anthu anga adzakhuta ndi zabwino zanga,”
akutero Yehova.
15 Yehova akuti,
“Kulira kukumveka ku Rama,
kulira kwakukulu,
Rakele akulirira ana ake.
Sakutonthozeka
chifukwa ana akewo palibe.”
16 Yehova akuti,
“Leka kulira
ndi kukhetsa misozi
pakuti udzalandira mphotho ya ntchito yako,”
akutero Yehova.
“Iwo adzabwerako ku dziko la adani.
17 Tsono chiyembekezo chilipo pa zamʼtsogolo,”
akutero Yehova.
“Ana ako adzabwerera ku dziko lawo.
 
18 “Ndithu ndamva Efereimu akubuwula kuti,
‘Ife tinali ngati ana angʼombe osamva.
Koma inu mwatiphunzitsa kumvera.
Mutibweze kuti tithe kubwerera,
chifukwa ndinu Yehova Mulungu wanga.
19 Popeza tatembenuka mtima,
ndiye tikumva chisoni;
popeza tazindikira
ndiye tikudziguguda pachifukwa.
Tachita manyazi ndipo tanyazitsidwa
chifukwa tinachimwa paubwana wathu.’
20 Kodi Efereimu si mwana wanga wokondedwa,
mwana amene Ine ndimakondwera naye?
Ngakhale nthawi zambiri ndimamudzudzula,
ndimamukumbukirabe.
Kotero mtima wanga ukumufunabe;
ndimamumvera chifundo chachikulu kwambiri,”
akutero Yehova.
 
21 “Muyike zizindikiro za mu msewu;
muyimike zikwangwani.
Yangʼanitsitsani msewuwo,
njira imene mukuyendamo.
Bwerera, iwe namwali wa Israeli,
bwerera ku mizinda yako ija.
22 Udzakhala jenkha mpaka liti,
iwe mwana wa mkazi wosakhulupirika?
Yehova walenga chinthu chatsopano pa dziko lapansi; mkazi ndiye tsopano aziteteza mwamuna.”
23 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Ndikadzabwera nawo anthuwa kuchokera ku ukapolo, anthu a mʼdziko la Yuda ndi amene akukhala mʼmizinda yake adzayankhulanso mawu akuti, ‘Yehova akudalitse, iwe malo achilungamo, iwe phiri lopatulika.’ 24 Anthu adzakhala ku Yuda ndi ku mizinda yake pamodzi ndi alimi ndi oweta nkhosa. 25 Ndidzatsitsimutsa anthu otopa ndipo ndidzadyetsa anthu anjala.”
26 Pamenepo ndinadzuka nʼkuyangʼana uku ndi uku. Tulo tanga tinali tokoma.
27 “Masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzachulukitsa anthu pamodzi ndi ziweto mʼdziko la Israeli ndi la Yuda. 28 Monga momwe ndinasamalira powazula, powagwetsa, powagumula, powawononga ndi powachita zoyipa, momwemonso ndidzasamala powamanga ndi powadzala” akutero Yehova. 29 “Mʼmasiku amenewo anthu sadzanenanso kuti,
“Makolo adya mphesa zosapsa,
koma mano a ana ndiye achita dziru.
30 Mʼmalo wake, munthu aliyense adzafa chifukwa cha tchimo lake. Iye amene adzadye mphesa zosapsazo ndiye amene mano ake adzachite dziru.”
31 “Masiku akubwera,” akutero Yehova,
“pamene ndidzachita pangano latsopano
ndi Aisraeli
ndiponso nyumba ya Yuda.
32 Silidzakhala ngati pangano
limene ndinachita ndi makolo awo
pamene ndinawagwira padzanja
nʼkuwatulutsa ku Igupto;
chifukwa anaphwanya pangano langa,
ngakhale ndinali mwamuna wawo,”
akutero Yehova.
33 “Ili ndi pangano limene ndidzachita ndi Aisraeli
atapita masiku amenewo,” akutero Yehova.
“Ndidzayika lamulo langa mʼmitima mwawo
ndi kulilemba mʼmaganizo mwawo.
Ine ndidzakhala Mulungu wawo
ndipo iwo adzakhala anthu anga.
34 Sipadzafunikanso kuti wina aphunzitse mnzake,
kapena munthu wina kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, ‘Mudziwe Yehova,’
chifukwa onse adzandidziwa Ine,
kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,”
akutero Yehova.
“Ndidzawakhululukira zoyipa zawo
ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”
35 Yehova akuti,
Iye amene amakhazikitsa dzuwa
kuti liziwala masana,
amene amalamula kuti mwezi ndi nyenyezi
ziziwala usiku,
amene amavundula nyanja
kuti mafunde akokome,
dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:
36 Ngati zimenezi zilekeka pamaso panga, akutero Yehova, pamenepo padzakhala pamathero a fuko la Israeli pamaso panga.
37 Yehova akuti,
“Ndidzataya fuko la Israeli chifukwa cha machimo awo.
Ngati patapezeka munthu
amene angathe kupima zakuthambo
nʼkufufuza maziko a dziko lapansi.”
38 “Taonani masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene mzinda wa Yehova udzamangidwanso kuyambira ku Nsanja ya Hananeli mpaka ku Chipata cha Ngodya. 39 Malire ake adzayambira pamenepo kupita ku phiri la Garebu, nʼkudzakhota kuloza ku Gowa. 40 Chigwa chonse mʼmene amatayiramo mitembo ndi phulusa, ndiponso minda yonse kuyambira ku Chigwa cha Kidroni mpaka ku ngodya ya Chipata cha Akavalo mbali ya kummawa, adzakhala malo opatulika a Yehova. Mzindawu sadzawuzulanso kapena kuwuwononga.”