29
Kalata Yolembera Anthu a ku Ukapolo
1 Yeremiya anatumiza kalata kuchokera ku Yerusalemu kupita kwa akuluakulu amene anali ku ukapolo, ndiponso kwa ansembe, aneneri pamodzi ndi anthu onse amene Nebukadinezara anawatenga ku Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. 2 Zimenezi zinachitika mfumu Yekoniya, amayi a mfumu, nduna za mfumu ndiponso atsogoleri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu, anthu aluso ndi amisiri atatengedwa ku Yerusalemu kupita ku ukapolo. 3 Yeremiya anapatsira kalatayo Eleasa mwana wa Safani ndi Gemariya mwana wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatumiza kwa Mfumu Nebukadinezara ku Babuloni. Mʼkalatamo analembamo kuti:
4 Anthu onse amene anatengedwa ukapolo kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Babuloni, Yehova akuwawuza kuti, 5 “Mangani nyumba ndipo muzikhalamo. Limani minda ndipo mudye zipatso zake. 6 Kwatirani ndipo mubereke ana aamuna ndi aakazi. Ana anu aamuna muwasankhire akazi ndipo muwasankhire amuna ana anu aakaziwo, kuti nawonso abale ana aamuna ndi aakazi. Muchulukane kumeneko. Chiwerengero chanu chisachepe. 7 Ndiponso muzifunafuna mtendere ndi ubwino wa mzinda umene ndinakupirikitsirani ku ukapoloko. Muzipempherera mzindawo kwa Yehova, kuti zikuyendereni bwino.” 8 Inde, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, “Musalole kuti aneneri ndi owombeza amene ali pakati panu akunyengeni. Musamvere maloto awo. 9 Iwo akunenera zabodza kwa inu mʼdzina langa ngakhale Ine sindinawatume,” akutero Yehova.
10 Yehova akuti, “Zaka 70 za ku Babuloni zikadzatha, ndidzabwera kudzakuchitirani zabwino zonse zimene ndinakulonjezani zija, ndipo ndidzakubwezerani ku malo ano. 11 Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani,” akutero Yehova, “ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo. 12 Nthawi imeneyo mudzandiyitana, ndi kunditama mopemba ndipo ndidzakumverani. 13 Mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza. Mukadzandifuna ndi mtima wanu wonse 14 mudzandipezadi,” akutero Yehova, “ndipo ndidzakubwezerani zabwino zanu. Ndidzakusonkhanitsani kuchokera ku mayiko onse ndi kumalo konse kumene munali,” akutero Yehova, “ndipo ndidzakubweretsani kumalo kumene munali ndisanakuchotseni kukupititsani ku ukapolo.”
15 Inu mumati, “Yehova watiwutsira aneneri athu ku Babuloni,” 16 koma zimene Yehova akunena za mfumu imene ikukhala pa mpando waufumu wa Davide pamodzi ndi anthu onse amene anatsala mu mzinda muno, abale anu amene sanapite nanu ku ukapolo ndi izi, 17 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndidzawapha ndi nkhondo, njala ndi mliri ndipo ndidzawasandutsa ngati nkhuyu zowola kwambiri, zosati nʼkudya. 18 Ndidzawalondola ndi lupanga, njala ndi mliri ndipo ndidzawasandutsa chinthu chonyansa kwa anthu amayiko onse a pa dziko lapansi. Adzakhala otembereredwa, ochititsa mantha, onyozeka ndiponso ochitidwa chipongwe pakati pa anthu a mitundu yonse kumene ndawapirikitsirako. 19 Zidzatero chifukwa sanamvere mawu anga amene ndinkawatumizira kudzera mwa atumiki anga, aneneri. Ngakhale inu amene muli ku ukapolo simunamverenso,” akutero Yehova.
20 Choncho, imvani mawu a Yehova, inu akapolo nonse amene ndinakuchotsani mu Yerusalemu ndi kukupititsani ku Babuloni. 21 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti zokhudza Ahabu mwana wa Kolaya ndi Zedekiya mwana wa Maseya, amene akulosera zabodza kwa inu mʼdzina langa: “Taonani ndidzawapereka kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo adzawapha inu mukupenya. 22 Chifukwa cha anthu awiriwo, akapolo onse ochokera ku Yuda amene ali ku Babuloni adzagwiritsa ntchito mawu awa potemberera: ‘Yehova achite nawe monga mmene anachitira ndi Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babuloni inawatentha.’ 23 Pakuti anthu amenewa achita zoyipa kwambiri mu Israeli; achita chigololo ndi akazi a eni ake ndipo mʼdzina langa ankayankhula zabodza zimene sindinawawuze kuti atero. Ine ndikuzidziwa ndipo ndine mboni ya zimenezi,” akutero Yehova.
Kalata ya Semaya
24 Ukamuwuze Semaya wa ku Nehelamu kuti, 25 “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Iwe unatumiza kalata mʼdzina lako kwa anthu onse a mu Yerusalemu, kwa Zefaniya mwana wa wansembe Maseya, ndi kwa ansembe onse. Unalemba mu kalatayo kuti, 26 ‘Yehova wakusankha kukhala wansembe mʼmalo mwa Yehoyada kuti ukhale wamkulu woyangʼanira Nyumba ya Yehova. Munthu aliyense wamisala amene akudziyesa kuti ndi mneneri uzimuponya mʼndende ndi kumuveka goli lachitsulo. 27 Nanga tsono chifukwa chiyani simunamuchitire zimenezi Yeremiya wa ku Anatoti, amene amakhala ngati mneneri pakati panu? 28 Yeremiyayo watitumizira uthenga uwu kuno ku Babuloni: Ukapolo wanu ukhala wa nthawi yayitali. Choncho mangani nyumba ndipo muzikhalamo; limani minda ndipo mudye zipatso zake.’ ”
29 Koma wansembe Zefaniya anayiwerenga kalatayo pamaso pa mneneri Yeremiya. 30 Ndipo Yehova anawuza Yeremiya kuti, 31 “Tumiza uthenga uwu kwa akapolo onse: ‘Yehova akuti zokhudza Semaya wa ku Nehelamu: Semaya wakuloserani, ngakhale kuti Ine sindinamutume, ndipo wakunyengani kuti muzikhulupirira bodza. 32 Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti: Mʼbanja lakelo sipadzakhala munthu pakati pa mtundu uno wa anthu amene adzaone zinthu zabwino zimene ndidzachitira anthu anga chifukwa analalika zondiwukira,’ ” akutero Yehova.