16
Sarai ndi Hagara
Tsono Sarai, mkazi wa Abramu anali asanamuberekere ana Abramuyo. Koma anali ndi wantchito wamkazi wa ku Igupto dzina lake Hagara; ndipo Sarai anati kwa Abramu, “Yehova sanalole kuti ine ndikhale ndi ana. Bwanji mulowe mwa wantchito wanga wamkaziyu kuti mwina ndingaone ana kudzera mwa iyeyu.”
Abramu anamvera Sarai. Tsono Sarai anatenga Hagara wantchito wake wamkazi wa ku Igupto uja namupereka kwa Abramu mwamuna wake kuti akhale mkazi wake. Izi zinachitika Abramu atakhala ku Kanaani zaka khumi. Abramu atalowana ndi Hagara, Hagara uja anatenga mimba.
Pamene Hagara anadziwa kuti anali woyembekezera anayamba kunyoza mbuye wake Sarai. Pamenepo Sarai anati kwa Abramu, “Inu ndinu amene mwandiputira nkhanza zikundichitikirazi. Ndinakupatsani wantchito wanga wamkazi kuti akhale mkazi wanu, ndiye tsopano wayamba kundinyoza ine chifukwa wadziwa kuti ndi woyembekezera. Yehova ndiye amene aweruze pakati pa inu ndi ine.”
Abramu anati, “Wantchito wakoyu ali mʼmanja mwako. Chita naye chilichonse chimene ukuganiza kuti ndi chokukomera.” Tsono Sarai anazunza Hagara mpaka anathawa.
Mngelo wa Yehova anamupeza Hagara pafupi ndi chitsime mʼchipululu. Chinali chitsime chimene chili mʼmphepete mwa msewu wopita ku Suri. Ndipo mngeloyo anati, “Hagara, iwe wantchito wa Sarai, ukuchokera kuti ndipo ukupita kuti?”
Iye anayankha, “Ndikuthawa mbuye wanga Sarai.”
Mngelo wa Yehova anamuwuza kuti, “Bwerera kwa mbuye wako ndipo ukamugonjere. 10 Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri zoti munthu sangaziwerenge.”
11 Mngelo wa Yehova uja anamuwuzanso kuti,
“Ndiwe woyembekezera
ndipo udzabala mwana wamwamuna.
Udzamutcha dzina lake Ismaeli,
pakuti Yehova wamva kulira chifukwa cha kuzunzika kwako.
12 Iye adzakhala munthu wa khalidwe ngati mʼmbulu wamisala;
adzadana ndi aliyense
ndipo anthu onse adzadana naye,
adzakhala mwaudani pakati pa abale ake
onse.”
13 Hagara anatcha Yehova amene anamuyankhula uja dzina loti: “Ndinu Mulungu amene mumandiona,” popeza anati, “Ndakumana ndi Yehova atatha kundikomera mtima.” 14 Nʼchifukwa chake chitsime chija chimene chili pakati pa Kadesi ndi Beredi chinatchedwa Beeri-lahai-roi.
15 Tsono Hagara anamuberekera Abramu mwana wamwamuna ndipo Abramu anamutcha mwanayo Ismaeli. 16 Pamene Hagara anamubalira Ismaeli nʼkuti Abramuyo ali ndi zaka 86.