23
Wosayenera mu Msonkhano
1 Mwamuna aliyense wofulidwa kapena woduka chiwalo chachimuna asalowe nawo mu msonkhano wa Yehova.
2 Aliyense wobadwa mʼbanja losavomerezeka, kapena mdzukulu wake wina aliyense, ngakhale mibado khumi pambuyo pake, asalowe mu msonkhano wa Yehova.
3 Mwamoni kapena Mmowabu asalowe mu msonkhano wa anthu a Yehova ngakhale mibado khumi yobwera pambuyo pake. 4 Pakuti iwowa sanabwere kudzakulonjerani ndi chakudya kapena madzi pamene mumadutsa pochokera ku Igupto, mʼmalo mwake anakalemba ganyu Balaamu mwana wa Beori wochokera ku Petori ku Mesopotamiya kuti akutemberereni. 5 Komabe Yehova Mulungu wanu sanamvere Balaamu koma anatembenuza temberero kukhala dalitso kwa inu chifukwa Yehova Mulungu wanu amakukondani. 6 Musachite nawo mgwirizano uliwonse wa mtendere pa moyo wanu wonse.
7 Musapeputse Mwedomu pakuti ndi mʼbale wanu ndithu. Musapeputse Mwigupto chifukwa munali alendo mʼdziko lake. 8 Mʼbado wachitatu wa ana awo akhoza kulowa mu msonkhano wa anthu a Yehova.
Masamalidwe a Msasa
9 Mukamakhala pa msasa pokonzekera adani anu, musayandikane ndi china chilichonse chodetsedwa. 10 Wina mwa asilikali anu akadziwonongera ndi umuna usiku, ayenera kuchoka pa msasapo ndipo akhale kunja kwa msasa. 11 Koma dzuwa likapendeka ayenera kusamba ndipo polowa dzuwa akhoza kubwerera ku msasa.
12 Mukonze malo kunja kwa msasa kumene mukhoza kukadzithandizirako. 13 Pakati pa zida zanu muzikhala ndi china chokumbira, ndipo pokadzithandiza muzikumba kadzenje ndi kukwirira chimbudzi chanu. 14 Pakuti Yehova Mulungu wanu amayendayenda ku msasa wanu kukutchinjirizani ndi kupereka adani anu kwa inu. Nʼchifukwa chake msasa wanu uzikhala wopatulika kuti mwina angaone china chonyansa nabwerera osakuyandikirani.
Malamulo Osiyanasiyana
15 Ngati kapolo wathawa mbuye wake nakabisala kwanu, musamuperekenso kwa mbuye wakeyo. 16 Mumulole akhale pakati panu, paliponse pamene angakonde, mʼmudzi umene angasankhe ndipo musamupondereze.
17 Pasapezeke Mwisraeli wamwamuna kapena wamkazi wochita chiwerewere ku Nyumba ya Mulungu. 18 Musabweretse malipiro a wachiwerewere wamkazi kapena wamwamuna Mʼnyumba ya Yehova Mulungu wanu kudzapereka za malumbiro aliwonse, chifukwa Yehova Mulungu wanu amadana ndi zimenezi.
19 Musamalipitse mʼbale wanu chiwongoladzanja, kaya pa ndalama, kapena pa chakudya, kapena pa china chilichonse choti nʼkupereketsa chiwongoladzanja. 20 Mlendo mukhoza kumulipitsa chiwongoladzanja koma osati mʼbale wanu Mwisraeli, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa zochitika zanu zonse mʼdziko mukulowamoli.
21 Mukalumbira kupereka kanthu kwa Yehova Mulungu wanu, musamachedwetse kupereka, chifukwa Yehova Mulungu wanu adzakufunsanibe kanthuko ndipo mudzapezeka wochimwa. 22 Koma ngati mupewa kupanga mapangano simudzapezeka ochimwa. 23 Zilizonse zimene mulumbira ndi pakamwa panu muzitsimikiza kuzichita, chifukwa mwalumbira mwaufulu pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi pakamwa panu.
24 Mukalowa mʼmunda wamphesa wa mnzanu mukhoza kudya mphesa mmene mungafunire koma musayike zina mʼdengu mwanu. 25 Mukalowa mʼmunda wa tirigu wa mʼbale wanu, mukhoza kutengako ngala mʼmanja mwanu, koma osasenga tirigu ndi chikwakwa.