18
Ku Korinto
1 Zitatha izi, Paulo anachoka ku Atene ndipo anapita ku Korinto. 2 Kumeneko anakumana ndi Myuda wina dzina lake Akula, nzika ya ku Ponto amene anali atangofika kumene kuchokera ku Italiya pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudiyo analamula Ayuda onse kuti achoke ku Roma. Paulo anapita kukawaona. 3 Popeza Paulo anali mʼmisiri wosoka matenti monga iwo, iye anakhala nawo namagwirira ntchito pamodzi. 4 Tsiku la Sabata lililonse Paulo amakambirana ndi anthu mʼsunagoge, kufuna kukopa Ayuda ndi Agriki.
5 Sila ndi Timoteyo atafika kuchokera ku Makedoniya, Paulo ankangogwira ntchito yolalikira yokha basi, kuchitira umboni Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu. 6 Koma pamene Ayuda anatsutsana naye ndi kumuchita chipongwe, iye anakutumula zovala zake nati, “Magazi anu akhale pamitu yanu! Ine ndilibe mlandu. Kuyambira tsopano ndipita kwa anthu a mitundu ina.”
7 Ndipo Paulo anatuluka mʼsunagoge napita ku nyumba yoyandikana ndi sunagoge ya Tito Yusto, munthu wopembedza Mulungu. 8 Krispo, mkulu wa sunagoge, pamodzi ndi a pa banja lake lonse anakhulupirira Ambuye; ndiponso Akorinto ambiri amene anamva Paulo akulalikira anakhulupiriranso nabatizidwa.
9 Usiku wina Ambuye anaonekera kwa Paulo mʼmasomphenya namuwuza kuti, “Usaope, pitiriza kuyankhula, usakhale chete. 10 Pakuti Ine ndili nawe, palibe aliyense amene adzakukhudza ndi kukuchitira choyipa, chifukwa mu mzinda muno ndili ndi anthu ambiri.” 11 Choncho Paulo anakhala kumeneko chaka ndi miyezi isanu ndi umodzi akuphunzitsa Mawu a Mulungu.
12 Galiyo ali mkulu wa boma wa ku Akaya, Ayuda mogwirizana anamugwira Paulo napita naye ku bwalo la milandu. 13 Iwo anati, “Munthu uyu akukopa anthu kuti azipembedza Mulungu mwanjira zotsutsana ndi malamulo athu.”
14 Pamene Paulo ankati ayankhule, Galiyo anati kwa Ayuda, “Ukanakhala mlandu wochita choyipa kapena wolakwira mnzake, bwenzi nditakumverani bwinobwino. 15 Koma popeza ndi nkhani yokhudza mawu, mayina ndi malamulo anu, kambiranani nokhanokha. Ine sindidzaweruza zinthu zimenezi.” 16 Kotero iye anawapirikitsa mʼbwalo la milandu. 17 Kenaka iwo anagwira Sositene, mkulu wa sunagoge, ndipo anamumenya mʼbwalo la milandu momwemo. Koma Galiyo sanasamale zimenezi.
Prisila, Akula ndi Apolo
18 Paulo anakhalabe ku Korinto masiku ambiri. Kenaka anawasiya abale nakwera sitima ya pamadzi kupita ku Siriya, pamodzi ndi Prisila ndi Akula. Asanakakwere sitima ya pamadzi, anameta tsitsi lake ku Kenkreya chifukwa anali atalumbira. 19 Iwo anafika ku Efeso, kumene Paulo anasiyako Prisila ndi Akula. Iye yekha analowa mʼsunagoge nakambirana ndi Ayuda. 20 Iwo atapempha kuti akakhale nawo nthawi yayitali, iye anakana. 21 Koma pamene amachoka anawalonjeza kuti, “Ndidzabweranso Mulungu akalola.” Ndipo anakwera sitima ya pamadzi kuchoka ku Efeso. 22 Pamene Paulo anafika ku Kaisareya, anakwera kukapereka moni ku mpingo kenaka anatsikira ku Antiokeya.
23 Atakhala kwa kanthawi ku Antiokeya, Paulo anachokako nayendera madera onse a ku Galatiya ndi ku Frugiya kulimbikitsa ophunzira onse.
Za Apolo
24 Pa nthawi yomweyi Myuda wina dzina lake Apolo, mbadwa ya ku Alekisandriya anafika ku Efeso. Anali munthu wophunzira ndi wodziwa bwino Malemba. 25 Apoloyu anaphunzitsidwa njira ya Ambuye, ndipo anayankhula ndi changu chachikulu naphunzitsa za Yesu molondola, ngakhale amadziwa ubatizo wa Yohane wokha. 26 Iye anayamba kuyankhula mʼsunagoge molimba mtima. Pamene Prisila ndi Akula anamva, iwo anamuyitanira ku nyumba yawo ndipo anamufotokozera njira ya Mulungu molongosoka bwino.
27 Pamene Apolo anafuna kupita ku Akaya, abale anamulimbikitsa, nalemba kalata kwa ophunzira a kumeneko kuti amulandire. Atafika kumeneko, anathandiza kwambiri amene anakhulupirira mwachisomo. 28 Pakuti iye anatsutsa Ayuda mwamphamvu pamaso pa anthu, natsimikiza kuchokera mʼMalemba kuti Yesu ndiye Khristu.