19
1 Yowabu anawuzidwa kuti, “Mfumu ikulira maliro a Abisalomu.” 2 Ndipo kwa asilikali onse chipambano cha tsiku limenelo chinasandulika maliro, chifukwa tsiku limenelo anthu anamva kuti mfumu ili pa chisoni chachikulu chifukwa cha mwana wake. 3 Ankhondo analowa mu mzinda mwakachetechete tsiku limenelo ngati momwe amalowera anthu mwamanyazi chifukwa athawa ku nkhondo. 4 Mfumu inaphimba nkhope yake ndipo inalira mofuwula, “Iwe mwana wanga Abisalomu! Iwe Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!”
5 Kenaka Yowabu analowa mʼnyumba ya mfumu nafika kwa mfumuyo ndipo anati, “Lero mwachititsa manyazi asilikali anu onse, amene apulumutsa moyo wanu ndiponso moyo wa ana anu aamuna ndi aakazi, kudzanso moyo wa akazi anu ndi wa azikazi anu. 6 Inu mumakonda amene amadana nanu ndipo mumadana ndi amene amakukondani. Inuyo mwaonetsa lero poyera kuti simusamala za atsogoleri anu a nkhondo ndi asilikali awo. Ine ndikuona kuti inu mukanakondwera ngati Abisalomu akanakhala ndi moyo lero, tonsefe titafa. 7 Tsopano pitani mukawalimbikitse asilikali anu. Ine ndikulumbira mwa Yehova kuti ngati inu simupita palibe munthu amene adzatsale ali ndi inu polowa dzuwa. Ichi chidzakhala choyipa kwambiri kuposa zovuta zonse zimene zinakugwerani kuyambira muli mnyamata mpaka lero.”
8 Kotero mfumu inanyamuka ndipo inakhala pa mpando wake pa chipata. Pamene asilikali anawuzidwa kuti, “Mfumu yakhala pa chipata,” onse anabwera kwa iye.
Davide Abwerera ku Yerusalemu
Nthawi imeneyi nʼkuti Aisraeli atathawira ku nyumba zawo. 9 Pakati pa mafuko onse a Israeli, anthu amakangana ndipo amati, “Mfumu inatipulumutsa mʼmanja mwa adani anthu. Iye ndi amene anatilanditsa mʼdzanja la Afilisti. Koma tsopano wathawa mʼdziko muno chifukwa cha Abisalomu. 10 Ndipo Abisalomu amene ife tinamudzoza kuti atilamulire wafa pa nkhondo. Tsono nʼchifukwa chiyani simukunena kanthu za kubweretsanso mfumu?”
11 Mfumu Davide inatumiza uthenga uwu kwa ansembe Zadoki ndi Abiatara, “Funsani akuluakulu a Yuda, ‘Nʼchifukwa chiyani inu mukukhala otsiriza kuyitana mfumu ku nyumba yake yaufumu, pakuti zimene zikunenedwa mu Israeli yense zamveka kwa mfumu ndi onse amene akukhala nayo. 12 Inu ndinu abale anga enieni, mafupa anga ndi mnofu wanga. Nʼchifukwa chiyani inuyo mukukhala otsiriza kubweretsa mfumu?’ 13 Ndipo munene kwa Amasa, ‘Kodi iwe si mʼbale wanga weniweni? Mulungu andilange, andilange kwambiri ngati kuyambira tsopano sukhala mtsogoleri wa ankhondo anga kulowa mʼmalo mwa Yowabu.’ ”
14 Davide anakopa mitima ya anthu onse a Yuda ndipo anthuwo anakhala ngati munthu mmodzi. Iwo anatumiza mawu kwa mfumu, “Bwererani inu ndi anthu anu onse.” 15 Kotero mfumu inabwerera ndipo inakafika mpaka ku Yorodani.
Tsono anthu a ku Yuda anabwera ku Giligala kuti akakumane ndi mfumu ndi kumuwolotsa Yorodani. 16 Simei mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, anabwera mofulumira pamodzi ndi Ayuda kudzakumana ndi mfumu Davide. 17 Iyeyo anali ndi anthu 1,000 a fuko la Benjamini pamodzi ndi Ziba, wantchito wa banja la Sauli ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu ndi antchito ake makumi awiri. Iwo anathamangira ku Yorodani kumene kunali mfumu. 18 Iwo anawoloka mtsinje kukatenga banja lonse la mfumu ndi kuchita zonse zimene mfumuyo imafuna.
Pamene Simei mwana wa Gera anawoloka Yorodani, anagwa pansi chafufumimba pamaso pa mfumu, 19 ndipo anati, “Mbuye wanga musaganizire za kulakwa kwanga. Musakumbukire zolakwa zimene mtumiki wanu anakuchitirani tsiku limene mbuye wanga mfumu mumachoka mu Yerusalemu. Mfumu musazikumbukirenso zimenezi. 20 Pakuti ine mtumiki wanu ndazindikira kuti ndachimwa. Koma lero ndabwera ngati woyamba wa nyumba ya Yosefe yonse kudzakumana nanu mbuye wanga mfumu.”
21 Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati, “Kodi Simei saphedwa chifukwa cha ichi? Iye anatukwana wodzozedwa wa Yehova.”
22 Davide anayankha kuti, “Kodi inu ana a Zeruya, ndikuchitireni chiyani? Lero lino iwe wakhala mdani wanga! Kodi wina aphedwe lero mu Israeli? Kodi ine sindikudziwa kuti lero ndine mfumu mu Israeli?” 23 Ndipo mfumu inati kwa Simei, “Iwe Simei suphedwa.” Ndipo mfumuyo inalonjeza ndi lumbiro.
24 Mefiboseti, mdzukulu wa Sauli, nayenso anabwera kudzakumana ndi mfumu. Kuyambira tsiku limene mfumu inachoka mpaka tsiku limene inabwerera mu mtendere, iye sanasambe mapazi kaya kumeta ndevu kapena kuchapa zovala zake. 25 Pamene anafika kuchokera ku Yerusalemu kudzakumana ndi mfumu, mfumu inamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani sunapite nane Mefiboseti?”
26 Iye anayankha kuti, “Mbuye wanga mfumu, pakuti ine wantchito wanu ndine wolumala. Ndinati, ‘Andikonzere chishalo cha bulu wanga ndipo ndidzakwera kuti ndipite ndi mfumu.’ Koma Ziba wantchito wanga anandilakwitsa. 27 Ndipo wayankhula zosinjirira za ine mtumiki wanu kwa inu mbuye wanga mfumu. Mbuye wanga mfumu ali ngati mngelo wa Mulungu ndipo chitani chimene chikukomerani. 28 Zidzukulu zonse za agogo anga sizinayenera chilichonse koma imfa kuchokera kwa inu mbuye wanga mfumu, koma inu munapereka malo kwa mtumiki wanu pakati pa amene amadya pa tebulo lanu. Tsono ine ndili ndi chiyaninso kuti ndipitirize kudandaula kwa mfumu?”
29 Mfumu inayankha kuti, “Uneneranji zambiri? Ine ndikulamula kuti iwe ndi Ziba mugawane minda.”
30 Mefiboseti anati kwa mfumu, “Muloleni atenge zonse, pakuti tsopano mbuye wanga mwafika kwanu mu mtendere.”
31 Barizilai Mgiliyadi anabweranso kuchokera ku Rogelimu kudzawoloka Yorodani ndi mfumu ndi kumuperekeza kuchokera kumeneko. 32 Tsono Barizilai anali wokalamba kwambiri, wa zaka makumi asanu ndi atatu. Iye ndi amene anapereka zinthu kwa mfumu pamene anali ku Mahanaimu pakuti anali wolemera kwambiri. 33 Mfumu inati kwa Barizilai, “Woloka nane ndipo ukakhale ndi ine mu Yerusalemu ndipo ineyo ndidzakusamalira.”
34 Barizilai anayankha mfumu kuti, “Kodi zakhala zaka zingati zoti ndikhale ndi moyo, kuti ndipite ku Yerusalemu ndi mfumu? 35 Ine tsopano ndili ndi zaka 80. Kodi ndingathe kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa? Kodi mtumiki wanu angathe kuzindikira kukoma kwa zimene akudya ndi kumwa? Kodi ndingathe kumva kuyimba kwa amuna ndi akazi? Nʼchifukwa chiyani wantchito wanu akakhale ngati katundu kwa mbuye wanga mfumu? 36 Koma ine mtumiki wanu ndingoyenda pangʼono kuti ndiwoloke Yorodani pamodzi ndi mfumu. Amfumu mungandipatsirenji mphotho yotere? 37 Muloleni, mtumiki wanu abwerere, kuti ndikafere kwathu pafupi ndi manda a abambo ndi amayi anga. Koma nayu mtumiki wanu Kimuhamu. Muloleni iye awoloke nanu mbuye wanga mfumu. Mumuchitire chilichonse chimene chikukomereni!”
38 Mfumu inati, “Kimuhamu adzawoloka ndi ine, ndipo ndidzamuchitira iye chilichonse chimene chidzakondweretsa iwe. Ndipo chilichonse chimene udzandipempha ine ndidzakuchitira.”
39 Kotero anthu onse anawoloka Yorodani ndipo kenaka mfumu inawoloka. Mfumu inapsompsona Barizilai ndi kumupatsa madalitso ndipo Barizilaiyo anabwerera kwawo.
40 Pamene mfumu inawolokera ku Giligala, Kimuhamu anawoloka naye. Ankhondo onse a Yuda ndi theka la ankhondo a Israeli onse anaperekeza mfumu.
41 Kenaka Aisraeli onse amabwera kwa mfumu nʼkumati kwa iye, “Nʼchifukwa chiyani abale athu, anthu a ku Ayuda, anakubani mfumu, nawoloka nanu Yorodani inu ndi banja lanu, pamodzi ndi anthu ake onse?”
42 Ayuda onse anayankha Aisraeli kuti, “Ife timachita zimenezi chifukwa mfumu ndi mʼbale wathu. Nʼchifukwa chiyani inu mwapsa mtima ndi zimenezi? Kodi ife tinadya chakudya chilichonse cha mfumu? Kodi chilipo chimene ife tatenga kukhala chathu?”
43 Aisraeli anayankha Ayuda kuti, “Ife ndi magawo khumi mwa mfumu imeneyi, ndipo kuwonjezera apo, ife tili ndi zinthu zambiri mwa Davide kuposa inu. Tsono nʼchifukwa chiyani mukutichita chipongwe? Kodi ife si amene tinayamba kunena za kubweretsa mfumu yathu?”
Koma anthu a Yuda anayankha mwaukali kwambiri kupambana anthu a ku Israeli.