7
Mwambo Wopereka Nyumba kwa Yehova
1 Solomoni atamaliza kupemphera, moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kutentha nsembe zopsereza ndi nsembe zina, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza Nyumba ya Mulunguyo. 2 Ansembe sanathe kulowa mʼNyumba ya Mulungu chifukwa munadzaza ulemerero wa Yehova. 3 Aisraeli onse ataona moto ukuchokera kumwamba ndi ulemerero wa Yehova pamwamba pa Nyumba ya Mulungu, anagwada poyalidwa miyalapo ndipo anagunditsa nkhope zawo pansi, ndi kulambira ndi kutamanda Yehova, ponena kuti,
“Iye ndi wabwino;
chikondi chake chikhala chikhalire”
4 Tsono mfumu ndi anthu onse anapereka nsembe pamaso pa Yehova. 5 Ndipo mfumu Solomoni anapereka nsembe ngʼombe 22,000, nkhosa ndi mbuzi 120,000. Kotero mfumu ndi anthu onse anachita mwambo wopereka Nyumba kwa Mulungu. 6 Ansembe anayimirira mʼmalo mwawo, monganso anachitira Alevi ndi zida zoyimbira za Yehova, zimene Davide anapanga zotamandira Yehova ndipo zimagwiritsidwa ntchito pamene amatamanda, ponena kuti, “Chikondi chake chikhale chikhalire.” Moyangʼanizana ndi Alevi, ansembe amaliza malipenga, ndipo Aisraeli onse anali atayimirira.
7 Solomoni anapatula malo a pakati pa bwalo kutsogolo kwa Nyumba ya Yehova ndipo pamenepo anapereka nsembe zopsereza ndi mafuta, zopereka za chiyanjano, chifukwa guwa lansembe lamkuwa limene anapanga panalibe malo woti nʼkuperekerapo nsembe zopsereza, nsembe za ufa ndi mafuta.
8 Choncho nthawi imeneyi, Solomoni anachita chikondwerero kwa masiku asanu ndi awiri pamodzi ndi Aisraeli onse. Unali msonkhano waukulu, kuyambira ku Lebo Hamati mpaka ku chigwa cha ku Igupto. 9 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu panali msonkhano, pakuti anachita mwambo wopereka guwa lansembe kwa masiku asanu ndi awiri ndi masiku enanso asanu ndi awiri achikondwerero. 10 Pa tsiku la 23 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, Solomoni anawuza anthu aja kuti apite kwawo. Anthu anali achimwemwe ndi okondwa mʼmitima mwawo chifukwa cha zinthu zabwino zimene Yehova anachitira Davide ndi Solomoni ndiponso anthu ake Aisraeli.
Yehova Aonekera Solomoni
11 Solomoni atatsiriza kumanga Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu ndi kukwaniritsa kuchita zonse zimene zinali mu mtima mwake pa Nyumba ya Yehova ndi nyumba yake yaufumu, 12 Yehova anamuonekera usiku ndipo anati:
“Ine ndamva pemphero lako ndipo ndadzisankhira malo ano kukhala Nyumba yanga yoperekeramo nsembe.
13 “Ine ndikatseka kumwamba kuti mvula isagwe, kapena kulamulira dzombe kuti liwononge dziko, kapena kutumiza mliri pakati pa anthu, 14 ngati anthu anga, amene amatchedwa ndi dzina langa adzichepetsa ndi kupemphera ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zawo zoyipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwamba ndipo ndidzakhululuka tchimo lawo ndi kuchiritsa dziko lawo. 15 Ndipo maso anga adzatsekuka ndi makutu anga adzakhala tcheru kumva mapemphero a pamalo pano. 16 Ine ndasankha ndipo ndapatula Nyumba yangayi kotero kuti ndidzakhala mʼmenemo kwamuyaya. Maso ndi mtima wanga zidzakhala pano nthawi zonse.
17 “Kunena za iwe, ukayenda pamaso panga mokhulupirika monga momwe anachitira abambo ako Davide, ndi kuchita zonse zimene ndakulamula, ndi kusamalitsa malangizo ndi malamulo anga, 18 Ine ndidzakhazikitsa mpando wako waufumu, monga ndinachitira pangano ndi abambo ako Davide pamene ndinati, ‘Sipadzasowa munthu wolamulira Israeli.’
19 “Koma ngati iwe udzapatuka ndi kutaya malangizo ndi malamulo amene ndakupatsa ndi kupita kukatumikira milungu ina ndi kuyipembedza, 20 pamenepo Ine ndidzazula Aisraeli mʼdziko langa limene ndinawapatsa, ndiponso ndidzayikana Nyumba ino imene ndadzipatulira. Ndipo udzakhala ngati mwambi ndi chinthu chonyozedwa pakati pa anthu onse. 21 Ndipo ngakhale kuti tsopano Nyumba ya Mulunguyi ndi yokongola kwambiri, onse amene adzadutsa pano adzadabwa kwambiri ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere mʼdziko muno ndi pa Nyumba ya Mulunguyi?’ 22 Anthu adzayankha kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti asiya Yehova, Mulungu wa makolo awo, amene anawatulutsa mʼdziko la Igupto ndipo akangamira milungu ina ndi kumayipembedza ndi kuyitumikira. Choncho Iye wabweretsa zovuta zonsezi.’ ”