4
Atumiki a Khristu
1 Choncho tsono anthu atione ife monga atumiki a Khristu, ndiponso ngati osunga zinsinsi za Mulungu. 2 Chofunika kwambiri nʼchakuti amene apatsidwa udindo oyangʼanira aonetse kukhulupirika. 3 Ine ndilibe nazo kanthu ngati ndiweruzidwa ndi inu kapena khothi lina lililonse. Ndithu, inenso sindidziweruza ndekha. 4 Chikumbumtima changa sichikunditsutsa, koma sikuti ndine wolungama. Wondiweruza ine ndi Ambuye. 5 Chomwecho musaweruze nthawi yoweruza isanakwane. Dikirani mpaka Ambuye atabwera. Iye adzaonetsa poyera zimene zabisika mu mdima ndipo adzaonetsa maganizo a mʼmitima ya anthu. Pa nthawi imeneyo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko.
6 Tsono abale, ndapereka chitsanzo cha ine mwini ndi Apolo kuti mupindule. Phunzirani kwa ife tanthauzo la mawu akuti, “Musamapitirire zimene Malemba akunena,” kuti musamanyade pamene wina aposa mnzake. 7 Pakuti ndani amakusiyanitsani ndi wina aliyense? Nʼchiyani muli nacho chimene simunalandire? Ndipo ngati munalandira, bwanji mumadzitukumula ngati kuti simunalandire?
8 Inu muli nazo kale zonse zimene mufuna! Inu mwalemera kale! Inu mwayamba kale kulamulira ife! Ndilakalaka mukanakhaladi mafumu kuti ife tikhale nawo mafumu pamodzi ndi inu. 9 Pakuti kwa ine zikuoneka ngati kuti Mulungu watiyika ife atumwi pachionetsero, kumapeto kwa mndandanda, monga anthu oweruzidwa kuti akaphedwe mʼmabwalo. Ife tayikidwa kuti tionekere ku dziko lonse, kwa angelo ndi anthu. 10 Ife ndife opusa chifukwa cha Khristu, koma inu ndinu anzeru mwa Khristu! Ife ndife ofowoka koma inu ndinu amphamvu! Inu ndinu olemekezeka koma ife ndife opeputsidwa! 11 Mpaka pano tili ndi njala ndi ludzu, tili ndi sanza, tikuzunzidwa, tilibe nyumba. 12 Timagwira ntchito molimbika ndi manja athu. Akamatitemberera, ife timadalitsa; tikasautsidwa, ife timapirira. 13 Pamene atilalatira timayankha mwachifundo. Mpaka pano takhala ngati zinyalala za dziko, monga zakudzala za dziko lapansi.
Pempho ndi Chenjezo
14 Sindikulemba izi kuti ndikuchititseni manyazi, koma kukuchenjezani monga ana anga okondedwa. 15 Ngakhale muli ndi anthu 10,000 okutsogolerani mwa Khristu, mulibe abambo ambiri, popeza mwa Khristu Yesu, ine ndakhala abambo anu kudzera mu Uthenga Wabwino. 16 Chifukwa chake ndikukupemphani kuti munditsanze ine. 17 Chifukwa cha ichi ndikutumiza kwa inu Timoteyo, mwana wanga amene ndimamukonda, amene ndi wokhulupirika mwa Ambuye. Adzakukumbutsani inuyo za moyo wanga mwa Khristu Yesu, umene ukugwirizana ndi zimene ndimaphunzitsa paliponse mu mpingo uliwonse.
18 Ena mwa inu mukudzitukumula, ngati kuti sindingabwere kwanu. 19 Koma ndibwera kwanuko posachedwapa, ngati Ambuye alola, ndipo ndi pamene ndidzadziwe osati zimene anthu odzitukumulawa akuyankhula, koma kuti mphamvu zawo nʼzotani. 20 Pakuti ufumu wa Mulungu si mawu chabe koma mphamvu. 21 Kodi musankha chiyani? Kodi ndidzabwere ndi chikwapu, kapena mu chikondi ndiponso mwa mzimu wofatsa?