19
Eliya Athawira ku Phiri la Horebu
Tsono Ahabu anawuza Yezebeli zonse zimene anachita Eliya ndi momwe anaphera aneneri onse ndi lupanga. Choncho Yezebeli anatuma mthenga kwa Eliya kuti akamuwuze kuti, “Milungu indilange, ndipo indilange koopsa, ngati mawa nthawi ngati yomwe ino sindidzakupha iwe monga unaphera aneneriwo.”
Eliya ataona zimenezi, ananyamuka nathawa kupulumutsa moyo wake. Atafika ku Beeriseba ku Yuda, anasiya mtumiki wake kumeneko, ndipo Eliyayo anayenda ulendo wa tsiku limodzi mʼchipululu. Anafika pa kamtengo ka tsache, nakhala pansi pa tsinde lake napemphera kuti afe. Iye anati, “Yehova, ine ndatopa nazo. Chotsani moyo wanga. Ineyo sindine wopambana makolo anga.” Ndipo Eliya anagona tulo tofa nato pa tsinde pa kamtengoko.
Ndipo taonani, mngelo anamukhudza, namuwuza kuti, “Dzuka udye.” Eliya anayangʼana, ndipo taonani kumutu kwake kunali buledi wootcha pa makala ndi botolo la madzi. Iye anadya ndi kumwa, nʼkugonanso.
Mngelo wa Yehova anabweranso kachiwiri, anamukhudza, namuwuza kuti, “Dzuka udye, popeza ulendowu ndi wautali.” Tsono Eliya anadzuka nadya ndi kumwa. Atapeza mphamvu chifukwa cha chakudyacho, anayenda masiku 40, usana ndi usiku mpaka anafika ku Horebu, phiri la Mulungu. Kumeneko analowa mʼphanga, nakhala komweko.
Ambuye Aonekera Eliya
Ndipo taonani, Yehova anayankhula naye kuti, “Eliya, ukuchita chiyani kuno?”
10 Iye anayankha kuti, “Ndakhala wodzipereka kwambiri kwa Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. Aisraeli asiya pangano lanu, agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga. Ndatsala ine ndekha ndipo tsopano akufuna kundipha.”
11 Yehova anati, “Tuluka ndipo ukayime pa phiri pamaso pa Yehova, pakuti Yehova ali pafupi kudutsa pamenepo.”
Tsono mphepo yayikulu ndi yamphamvu inawomba ningʼamba mapiri ndi kuswa matanthwe pamaso pa Yehova, koma Yehova sanali mʼmphepomo. Itapita mphepoyo panachita chivomerezi, koma Yehova sanali mʼchivomerezicho. 12 Chitapita chivomerezicho, panafika moto, koma Yehova sanali mʼmotomo. Ndipo utapita motowo, panamveka kamphepo kayaziyazi. 13 Eliya atamva kamphepoko, anakokera chovala chake naphimba kumutu. Anatuluka ndipo anayima pa khomo la phanga.
Ndipo panamveka mawu akuti, “Eliya, ukuchita chiyani kuno?”
14 Iye anayankha kuti, “Ndakhala wodzipereka kwambiri kwa Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. Aisraeli asiya pangano lanu, agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga. Ndatsala ine ndekha ndipo tsopano akufuna kundipha.”
15 Yehova anati kwa Eliyayo, “Bwerera njira imene unadzera, ndipo upite ku Chipululu cha ku Damasiko. Ukakafika kumeneko, ukadzoze Hazaeli kuti akhale mfumu ya ku Aramu. 16 Ukadzozenso Yehu mwana wa Nimisi kuti akhale mfumu ya Israeli, ndiponso ukadzoze Elisa mwana wa Safati wa ku Abeli-Mehola kuti akhale mneneri wolowa mʼmalo mwako. 17 Yehu adzapha aliyense amene adzapulumuke ku lupanga la Hazaeli, ndipo Elisa adzapha aliyense amene adzapulumuke ku lupanga la Yehu. 18 Komabe ndasunga anthu 7,000 ku Israeli, anthu onse amene mawondo awo sanagwadirepo Baala, onse amene pakamwa pawo sipanapsompsoneko fano lake.”
Kuyitanidwa kwa Elisa
19 Kotero Eliya anachoka kumeneko, nakapeza Elisa mwana wa Safati. Iye ankatipula ndi mapulawo khumi ndi awiri okokedwa ndi ngʼombe ziwiriziwiri zapamagoli, ndipo iye mwini ankayendetsa goli la khumi ndi chiwiri. Eliya anapita kumene anali namuveka chofunda chake. 20 Pomwepo Elisa anasiya ngʼombe zake nathamangira Eliya. Iye anati, “Mundilole kuti ndikatsanzike abambo ndi amayi anga, ndipo kenaka ndidzakutsatani.”
Eliya anayankha kuti, “Bwerera. Ine ndachita chiyani kwa iwe?”
21 Choncho Elisa anamusiya Eliyayo nabwerera kwawo. Anatenga ngʼombe zake ziwiri zapagoli nazipha. Anatenga magoli a mapulawo ake nasonkhera moto kuphikira nyamayo ndipo anayipereka kwa anthu kuti adye. Ndipo ananyamuka natsatira Eliya ndi kukhala mtumiki wake.